Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 53
  • Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira??

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira??
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yankho la m’Baibulo
  • Kodi Anthu Akafa Amapita Kudziko la Mizimu?
    Kodi Mizimu ya Akufa Ilipodi?
  • Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira?
    Galamukani!—2007
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Funso Lachiwiri: Kodi Chidzandichitikire N’chiyani Ndikadzamwalira?
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
ijwbq nkhani 53

Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira?

Yankho la m’Baibulo

Baibulo limanena kuti: “Amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse.” (Mlaliki 9:5; Salimo 146:4) Choncho tikamwalira timakhala kuti kulibeko. Munthu wakufa satha kuganiza, kuchita kanthu kapena kumva chilichonse.

“Kufumbiko udzabwerera”

Mulungu anafotokoza zimene zimachitika tikamwalira pamene analankhula ndi munthu woyambirira Adamu. Chifukwa chakuti Adamu sanamvere, Mulungu anamuuza kuti: “Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:19) Mulungu asanalenge Adamu “kuchokera kufumbi lapansi,” Adamuyo kunalibe. (Genesis 2:7) Choncho Adamu atamwalira, anabwerera kufumbi ndipo anasiya kukhala ndi moyo.

Izi ndi zimenenso zimachitikira anthu amene amamwalira masiku ano. Ponena za nyama ndi anthu omwe, Baibulo limati: “Zonse zinachokera kufumbi ndipo zonse zimabwerera kufumbi.”—Mlaliki 3:19, 20.

Anthu ena adzaukitsidwa

Baibulo nthawi zambiri limayerekezera imfa ndi tulo. (Salimo 13:3; Yohane 11:11-14; Machitidwe 7:60) Munthu amene akugona tulo tofa nato sadziwa zinthu zimene zikuchitika. N’chimodzimodzinso ndi akufa. Iwo sadziwa chilichonse. Komabe, Baibulo limatiuza kuti Mulungu ali ndi mphamvu zoukitsa akufa, ngati kuti anali m’tulo, kuti akhaleso ndi moyo. (Yobu 14:13-15) Kwa anthu amene Mulungu adzawaukitse, imfa sidzakhala mapeto a zonse.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena