11 Mawu Akuti “Chipangano Chakale” ndi “Chipangano Chatsopano”
2Ak 3:14—Chigiriki, ἐπὶ τῇ ἀναγνώσει τῆς παλαιᾶς διαθήκης (e·piʹ tei a·na·gnoʹsei tes pa·lai·asʹ di·a·theʹkes);
Chilatini, in lectione veteris testamenti
Anthu ambiri masiku ano amatchula Malemba amene kalelo analembedwa m’Chiheberi ndi m’Chiaramu, kuti “Chipangano Chakale.” Zimenezi zinachokera pa mmene mawu a pa 2Ak 3:14, anawalembera m’Baibulo lachilatini lotchedwa Vulgate ndi m’Baibulo la King James Version. Malemba Achigiriki anthu ambiri amawatcha kuti “Chipangano Chatsopano.” Tiyenera kukumbukira mfundo yakuti pa 2Ak 3:14, mawu achigiriki akuti di·a·theʹkes amatanthauza “pangano,” mofanana ndi m’malo ena 32 mmene mawuwa akupezeka m’Malemba Achigiriki.
Palemba limeneli, mtumwi Paulo sanali kunena za Malemba Achiheberi ndi Achiaramu onse pamodzi ayi. Ndipo sanali kutanthauza kuti malemba onse ouziridwa achikhristu ndi “chipangano chatsopano” ayi. Mtumwi Paulo anali kunena za pangano lakale la Chilamulo, limene linalembedwa ndi Mose m’mabuku oyambirira asanu a m’Baibulo. Mabukuwo ndi gawo chabe la Malemba onse amene analembedwa Chikhristu chisanayambe. N’chifukwa chake m’vesi lotsatira iye anati, “pamene zolemba za Mose zikuwerengedwa.”
Chotero, palibe chifukwa chomveka chotchulira Malemba Achiheberi ndi Achiaramu kuti “Chipangano Chakale,” kapena Malemba Achigiriki kuti “Chipangano Chatsopano.” Pofuna kutchula Malemba onse opatulika, ngakhale Yesu Khristu anali kunena kuti “Malemba.” (Mt 21:42; Mko 14:49; Yoh 5:39) Mtumwi Paulo anati “Malemba oyera,” ndiponso “Malemba.” (Aro 1:2; 15:4) Mogwirizana ndi mawu ouziridwa a pa Aro 1:2, Baibulo la Dziko Latsopano lili ndi mawu akuti “Malemba Opatulika” monga mbali ya mutu wake.