4 Mzimu
M’Malemba Achiheberi, mawu achiheberi akuti ruʹach (luwaki) akupezeka maulendo 260 kuyambira pa Ge 1:2. Mawuwa amatanthauza “mpweya umene munthu amatulutsa popuma,” koma alinso ndi matanthauzo ena kuwonjezera pamenepo. Matanthauzo onsewa akugwirizana pa mfundo imodzi iyi: Onse amanena za chinthu chosaoneka kwa anthu koma chimene chimasonyeza kuti pali mphamvu inayake imene ikugwira ntchito. Mphamvu yosaoneka imeneyo imatha kuchita zinthu zina zimene zimaoneka.
M’Malemba Achigiriki, mawu achigiriki akuti pneuʹma (penevuma) akupezeka maulendo 334, kuyambira pa Mt 1:18, pamene pakupezeka mawu akuti “mzimu woyera.” Mawu amenewa ndi ofanana matanthauzo ndi mawu achiheberi aja akuti ruʹach.
M’munsimu muli timitu tosiyanasiyana timene tikusonyeza malemba mmene mukupezeka mawu akuti ruʹach ndi pneuʹma.
Mphepo
Ge 8:1; Eks 10:13; 1Mf 18:45; Yoh 3:8.
Mzimu woyera, kapena Mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito
Ge 1:2; 41:38; Nu 11:25; Owe 6:34; 1Sa 19:20; 2Mb 24:20; Yes 11:2; Eze 11:5; Zek 4:6; Mt 1:18; 28:19; Mko 1:8; Lu 1:67; 2:27; Yoh 14:26; Mac 1:8; 2:33; Aro 5:5; 8:15, 16; 2Ak 13:14; Aef 3:16; 4:4; 1At 5:19; Tit 3:5; Yuda 20.
Mphamvu ya moyo
Ge 6:17; Yob 27:3; 34:14; Sl 31:5; 146:4; Mla 3:19; 12:7; Yes 42:5; Lu 8:55; 23:46; Mac 7:59.
Mulungu ndi mzimu, kapena wauzimu
Zolengedwa zauzimu
1Mf 22:21; Eze 3:12; 8:3; Mt 8:16; 10:1; Mko 3:11; 3:30; 1Ak 15:45; Ahe 1:7; 1Pe 3:18.
Kudzipereka, mtima, ndi maganizo
Ge 45:27; Eks 35:21; Nu 14:24; Yob 17:1; Miy 25:28; Yes 57:15; Da 2:1; Lu 1:17; Yoh 11:33; 13:21; Mac 17:16; 1Ak 16:18; 2Ak 2:13; 7:13; 1At 5:23.