Yobu
34 Elihu anapitiriza kulankhula kuti:
2 “Mvetserani mawu anga, anthu anzeru inu.
Ndipo anthu odziwa zinthu inu, ndimvereni.
4 Tiyeni tidzisankhire chiweruzo.
Tidziwe tokha pakati pathu chimene chili chabwino.
6 Kodi ndikunama za mmene chiweruzo changa chiyenera kukhalira?
Chilonda changa chachikulu sichikupola ngakhale kuti sindinachimwe.’+
8 Iye ndithu ali pa ulendo wokachita ubwenzi ndi anthu ochita zopweteka ena,
Komanso ali pa ulendo wokayenda ndi anthu oipa.+
10 Choncho inu amuna a mtima+ womvetsa zinthu, ndimvereni.
Mulungu woona sangachite zoipa m’pang’ono pomwe,+
Ndipo Wamphamvuyonse sangachite zinthu zopanda chilungamo ngakhale pang’ono.+
11 Pakuti iye amapereka mphoto kwa munthu wochokera kufumbi malinga ndi zochita zake,+
Ndipo amam’bweretsera zinthu zogwirizana ndi njira yake.
13 Ndani wam’patsa dziko lapansi?
Ndipo ndani wam’patsa ulamuliro panthaka yonse?
14 Akaika mtima wake pa munthu aliyense,
Akatenga mzimu* ndi mpweya wa munthuyo,+
15 Zamoyo zonse zimafera limodzi,
Ndipo munthu amabwerera kufumbi.+
16 Choncho ngati mumamvetsa zinthu, mvetserani izi.
Mvetserani mawu anga.
17 Kodi zoonadi munthu wodana ndi chilungamo angalamulire?+
Ngati munthu wamphamvu ali wolungama, kodi munganene kuti ndi woipa?+
18 Kodi munthu anganene kwa mfumu kuti, ‘Ndinu wopanda pake’?
Kapena angauze anthu olemekezeka kuti, ‘Ndinu oipa’?+
19 Alipo amene sanakonderepo akalonga,
Ndipo saganizira kwambiri wolemekezeka kuposa wonyozeka,+
Chifukwa onsewo anapangidwa ndi manja ake.+
20 Iwo amafa mwadzidzidzi,+ ngakhale pakati pa usiku.+
Anthuwo amagwedezeka uku ndi uku n’kufa,
Ndipo amphamvu amachoka popanda dzanja lowachotsa.+
23 Pakuti iye saikiratu nthawi yoti munthu aliyense
Apite kukaweruzidwa ndi Mulungu.
26 Amawamenya monga oipa,
Pamalo pomwe ena akuonerera.+
27 Chifukwa asiya kumutsatira,+
Ndipo sasamala za njira zake zonse,+
28 Kuti achititse kulira kwa wonyozeka kupita kwa iye.
Choncho iye amamva kulira kwa osautsika.+
29 Iye akachititsa bata, ndani angamudzudzule?
Ndipo akabisa nkhope yake,+ ndani angamuone?
Kaya abisire nkhope yake mtundu+ kapena munthu, n’chimodzimodzi.
31 Kodi munthu ndithu anganene kwa Mulungu kuti,
‘Ndapirira ngakhale kuti sindinachite cholakwa?+
32 Ngakhale kuti sindikuona chilichonse, inuyo ndiphunzitseni?
Ngati ndachita chosalungama chilichonse,
Sindidzachichitanso?’+
33 Kodi iye angakulipire mogwirizana ndi mmene ukuganizira, chifukwa chakuti ukukana chiweruzo chake?
Chifukwa chakuti iweyo wasankha wekha, osati ine?
Tsopano nena zimene ukudziwa.
34 Anthu a mtima womvetsa zinthu+ adzandiuza,
Ngakhale munthu wanzeru komanso wamphamvu amene akundimvetsera adzandiuza kuti,
35 ‘Yobu sadziwa zimene akunena,+
Ndipo amanena mawu osonyeza kuti iye ndi wosazindikira.’