Salimo 139:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Ndipo mdimawo sudzakhala mdima wandiweyani kwa inu,+Koma usiku udzakuwalirani ngati masana.+Mdima udzangokhala ngati kuwala.+ Yesaya 29:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Tsoka kwa anthu amene abisa patali kwambiri zolinga zawo, pozibisira Yehova,+ amene zochita zawo zimachitikira m’malo a mdima,+ ndipo amati: “Ndani akutiona, ndipo ndani akudziwa zimene tikuchita?”+ Yeremiya 23:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 “Kodi munthu aliyense angabisale m’malo obisika ine osamuona?”+ watero Yehova. “Kodi kumwamba kapena padziko lapansi, pali chilichonse chimene chingabisike kwa ine?”+ watero Yehova. Amosi 9:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Akabisala pamwamba pa phiri la Karimeli, ndidzawafufuza mosamala ndi kuwatenga,+ ndipo akathawa pamaso panga ndi kubisala pansi pa nyanja,+ ndidzalamula njoka pansi pa nyanja pomwepo kuti iwalume. Aheberi 4:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.+
12 Ndipo mdimawo sudzakhala mdima wandiweyani kwa inu,+Koma usiku udzakuwalirani ngati masana.+Mdima udzangokhala ngati kuwala.+
15 Tsoka kwa anthu amene abisa patali kwambiri zolinga zawo, pozibisira Yehova,+ amene zochita zawo zimachitikira m’malo a mdima,+ ndipo amati: “Ndani akutiona, ndipo ndani akudziwa zimene tikuchita?”+
24 “Kodi munthu aliyense angabisale m’malo obisika ine osamuona?”+ watero Yehova. “Kodi kumwamba kapena padziko lapansi, pali chilichonse chimene chingabisike kwa ine?”+ watero Yehova.
3 Akabisala pamwamba pa phiri la Karimeli, ndidzawafufuza mosamala ndi kuwatenga,+ ndipo akathawa pamaso panga ndi kubisala pansi pa nyanja,+ ndidzalamula njoka pansi pa nyanja pomwepo kuti iwalume.
13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.+