Genesis 16:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Ndiyeno Hagara anayamba kutchula dzina la Yehova n’kunena kuti: “Inu ndinu Mulungu amene amaona chilichonse.”*+ Anatinso: “Kodi nanenso pano ndaona wotha kundionayo?” Salimo 90:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Zolakwa zathu mwaziika patsogolo panu,+Ndipo machimo athu obisika* ali patsogolo pa nkhope yanu yowala.+ Salimo 139:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Ndingapite kuti kuthawa mzimu wanu,+Ndipo ndingapite kuti kuthawa nkhope yanu?+ Miyambo 15:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Maso a Yehova ali paliponse.+ Amayang’ana anthu oipa ndi abwino omwe.+ Amosi 9:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Akakumba Manda* kuti abisale mmenemo ndidzawatulutsa ndi dzanja langa,+ ndipo akakwera kumwamba ndidzawatsitsira pansi.+ Aheberi 4:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.+
13 Ndiyeno Hagara anayamba kutchula dzina la Yehova n’kunena kuti: “Inu ndinu Mulungu amene amaona chilichonse.”*+ Anatinso: “Kodi nanenso pano ndaona wotha kundionayo?”
8 Zolakwa zathu mwaziika patsogolo panu,+Ndipo machimo athu obisika* ali patsogolo pa nkhope yanu yowala.+
2 Akakumba Manda* kuti abisale mmenemo ndidzawatulutsa ndi dzanja langa,+ ndipo akakwera kumwamba ndidzawatsitsira pansi.+
13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.+