Yobu 34:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Pakuti maso ake amayang’anitsitsa njira za munthu,+Ndipo amaona mayendedwe ake onse. Salimo 11:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Yehova ali m’kachisi wake wopatulika.+Yehova, mpando wake wachifumu uli kumwamba.+Maso ake amaona, maso ake owala amasanthula+ ana a anthu. Salimo 66:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Iye akulamulira ndi mphamvu zake mpaka kalekale.+Maso ake akuyang’anitsitsa mitundu ya anthu.+Koma anthu oumitsa khosi asadzikweze.+ [Seʹlah.] Miyambo 5:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Pakuti njira za munthu zili pamaso pa Yehova,+ ndipo iye amaonetsetsa njira zake zonse.+ Yeremiya 16:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Pakuti maso anga akuona njira zawo zonse. Anthuwo sanabisike kwa ine, ndipo zolakwa zawo sizinabisike pamaso panga.+ Yeremiya 23:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 “Kodi munthu aliyense angabisale m’malo obisika ine osamuona?”+ watero Yehova. “Kodi kumwamba kapena padziko lapansi, pali chilichonse chimene chingabisike kwa ine?”+ watero Yehova. Aheberi 4:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.+
4 Yehova ali m’kachisi wake wopatulika.+Yehova, mpando wake wachifumu uli kumwamba.+Maso ake amaona, maso ake owala amasanthula+ ana a anthu.
7 Iye akulamulira ndi mphamvu zake mpaka kalekale.+Maso ake akuyang’anitsitsa mitundu ya anthu.+Koma anthu oumitsa khosi asadzikweze.+ [Seʹlah.]
17 Pakuti maso anga akuona njira zawo zonse. Anthuwo sanabisike kwa ine, ndipo zolakwa zawo sizinabisike pamaso panga.+
24 “Kodi munthu aliyense angabisale m’malo obisika ine osamuona?”+ watero Yehova. “Kodi kumwamba kapena padziko lapansi, pali chilichonse chimene chingabisike kwa ine?”+ watero Yehova.
13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.+