Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 6:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Pamenepo, Yehova anaona kuti kuipa kwa anthu kwachuluka padziko lapansi, ndipo malingaliro+ onse a m’mitima ya anthu anali oipa okhaokha nthawi zonse.+

  • 2 Mbiri 16:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Pajatu maso a Yehova+ akuyendayenda padziko lonse lapansi+ kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo+ uli wathunthu kwa iye. Mwachita zopusa+ pankhani imeneyi, chifukwa kuyambira tsopano anthu azichita nanu nkhondo.”+

  • Yobu 31:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Kodi iye saona njira zanga,+

      Ndi kuwerenga masitepe anga onse?

  • Miyambo 5:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Pakuti njira za munthu zili pamaso pa Yehova,+ ndipo iye amaonetsetsa njira zake zonse.+

  • Miyambo 15:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Maso a Yehova ali paliponse.+ Amayang’ana anthu oipa ndi abwino omwe.+

  • Yeremiya 16:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Pakuti maso anga akuona njira zawo zonse. Anthuwo sanabisike kwa ine, ndipo zolakwa zawo sizinabisike pamaso panga.+

  • Yeremiya 32:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Zolinga zanu ndi zazikulu+ ndipo zochita zanu ndi zambiri.+ Maso anu amaona njira zonse za ana a anthu+ kuti munthu aliyense mumuchitire zinthu mogwirizana ndi njira zake komanso zipatso za ntchito zake.+

  • 1 Petulo 3:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Pakuti maso+ a Yehova* ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzero lawo,+ koma nkhope ya Yehova imakwiyira anthu ochita zoipa.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena