10 Ine Yehova ndimafufuza mtima+ ndi kusanthula impso.+ Munthu aliyense ndimamuchitira zinthu monga mwa zochita zake,+ mogwirizana ndi zipatso za ntchito zake.+
19 Zolinga zanu ndi zazikulu+ ndipo zochita zanu ndi zambiri.+ Maso anu amaona njira zonse za ana a anthu+ kuti munthu aliyense mumuchitire zinthu mogwirizana ndi njira zake komanso zipatso za ntchito zake.+