2 Mbiri 16:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Pajatu maso a Yehova+ akuyendayenda padziko lonse lapansi+ kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo+ uli wathunthu kwa iye. Mwachita zopusa+ pankhani imeneyi, chifukwa kuyambira tsopano anthu azichita nanu nkhondo.”+ Yobu 34:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Pakuti maso ake amayang’anitsitsa njira za munthu,+Ndipo amaona mayendedwe ake onse. Salimo 33:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Kuchokera kumwamba, Yehova wayang’ana,+Waona ana onse a anthu.+ Salimo 66:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Iye akulamulira ndi mphamvu zake mpaka kalekale.+Maso ake akuyang’anitsitsa mitundu ya anthu.+Koma anthu oumitsa khosi asadzikweze.+ [Seʹlah.] Miyambo 5:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Pakuti njira za munthu zili pamaso pa Yehova,+ ndipo iye amaonetsetsa njira zake zonse.+ Miyambo 15:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Maso a Yehova ali paliponse.+ Amayang’ana anthu oipa ndi abwino omwe.+ Aheberi 4:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.+
9 Pajatu maso a Yehova+ akuyendayenda padziko lonse lapansi+ kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo+ uli wathunthu kwa iye. Mwachita zopusa+ pankhani imeneyi, chifukwa kuyambira tsopano anthu azichita nanu nkhondo.”+
7 Iye akulamulira ndi mphamvu zake mpaka kalekale.+Maso ake akuyang’anitsitsa mitundu ya anthu.+Koma anthu oumitsa khosi asadzikweze.+ [Seʹlah.]
13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.+