Miyambo
5 Mwana wanga, mvetsera nzeru zanga.+ Tchera makutu ako ku zimene ndikukuphunzitsa zokhudza kuzindikira,+ 2 kuti uteteze kuganiza bwino,+ ndiponso kuti milomo yako iteteze kudziwa zinthu.+
3 Pakuti milomo ya mkazi wachilendo imakha uchi ngati chisa cha njuchi+ ndipo m’kamwa mwake ndi mosalala kuposa mafuta.+ 4 Koma zotsatirapo zochokera kwa iye n’zowawa kwambiri ngati chitsamba chowawa.+ N’zakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.+ 5 Mapazi ake amatsikira ku imfa.+ Miyendo yake imalowera ku Manda.+ 6 Iye saganizira njira ya moyo.+ Amangoyendayenda panjira zake osadziwa kumene akupita.+ 7 Tsopano ananu ndimvereni,+ ndipo musapatuke pa mawu otuluka m’kamwa mwanga.+ 8 Njira yako ikhale kutali ndi iye. Usayandikire pakhomo la nyumba yake,+ 9 kuti usapereke ulemu wako kwa anthu ena+ kapena kupereka zaka zako ku zinthu zankhanza.+ 10 Ndiponso kuti alendo asakhute mphamvu zako,+ kuti zinthu zimene unazipeza movutikira* zisakhale m’nyumba ya mlendo,+ 11 komanso kuti usadzabuule m’tsogolo+ mnofu ndi thupi lako zikadzafika ku mapeto kwake.+ 12 Pa nthawiyo udzanena kuti: “Ndinkadana ndi malangizo* ine,+ ndipo mtima wanga sunkavomereza kudzudzula.+ 13 Sindinamvere mawu a alangizi anga,+ ndipo sindinatchere khutu kwa aphunzitsi anga.+ 14 N’chifukwa chake mosayembekezeka ndinagwera m’zinthu zoipa zamtundu uliwonse,+ ndipo ndinachita manyazi pamaso pa mpingo wonse.”+
15 Imwa madzi ochokera m’chitsime chako, komanso madzi oyenderera kuchokera pakati pa chitsime chako.+ 16 Kodi akasupe ako amwazike panja,+ ndipo mitsinje yako yamadzi imwazike m’mabwalo a mumzinda? 17 Zimenezi zikhale zako zokha osatinso za alendo amene ali nawe.+ 18 Kasupe wa madzi ako akhale wodalitsidwa,+ ndipo usangalale ndi mkazi wapaunyamata wako.+ 19 Iye akhale ngati mbawala yaikazi yokondedwa ndiponso ngati mbuzi yokongola ya m’mapiri.+ Mabere ake akukhutiritse nthawi zonse.+ Nthawi zonse uzikhala wokondwa kwambiri ndi chikondi chake.+ 20 Chotero pali chifukwa chanji choti usangalalire ndi mkazi wachilendo mwana wanga, kapena choti ukumbatirire chifuwa cha mkazi wina?+ 21 Pakuti njira za munthu zili pamaso pa Yehova,+ ndipo iye amaonetsetsa njira zake zonse.+ 22 Woipa adzagwidwa ndi zolakwa zake zomwe,+ ndipo adzamangidwa m’zingwe za tchimo lake lomwe.+ 23 Iye adzafa chifukwa chosamvera malangizo,+ ndiponso chifukwa chakuti amasocheretsedwa ndi zopusa zake zochuluka.+