Miyambo
1 Miyambi+ ya Solomo+ mwana wa Davide,+ mfumu ya Isiraeli,+ 2 yothandiza munthu kupeza nzeru+ ndi malangizo,*+ kuti amvetse mawu ozama,+ 3 kuti alandire malangizo+ amene amathandiza munthu kuzindikira,+ kuchita zolondola,+ zachilungamo+ ndi zowongoka.+ 4 Yothandiza kuti munthu wosadziwa akhale wochenjera,+kuti wachinyamata akhale wodziwa zinthu+ ndiponso kuti azitha kuganiza bwino.+
5 Munthu wanzeru amamvetsera ndi kuphunzira malangizo owonjezereka,+ ndipo munthu womvetsa zinthu ndi amene amapeza nzeru zoyendetsera moyo wake,+ 6 kuti azitha kumvetsa mwambi ndi mawu ozunguza mutu,+ mawu a anthu anzeru+ ndi mikuluwiko yawo.+
7 Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziwa zinthu.+ Nzeru ndi malangizo zimanyozedwa ndi zitsiru.*+
8 Mwana wanga, tamvera malangizo a bambo ako,+ ndipo usasiye malamulo a mayi ako,+ 9 pakuti zimenezi zili ngati nkhata ya maluwa yokongola pamutu pako,+ ndi mkanda wokongola m’khosi mwako.+
10 Mwana wanga, ochimwa akayesa kukunyengerera usavomere.+ 11 Akamanena kuti: “Tiye tipitire limodzi. Tiye tikabisalire anthu kuti tikakhetse magazi.+ Tiye tikabisalire anthu osalakwa. Tikachite zimenezo popanda chifukwa chilichonse.+ 12 Tiye tikawameze amoyo+ ngati mmene amachitira Manda,*+ tikawameze athunthu ngati amene akupita kudzenje.+ 13 Tiye tikapeze zinthu zamtengo wapatali zosiyanasiyana.+ Tiye tidzaze nyumba zathu ndi zofunkha.+ 14 Tiye tichitire limodzi maere. Tonsefe tikhale ndi chikwama chimodzi chokha.”+ 15 Mwana wanga, usayende nawo limodzi panjira.+ Letsa phazi lako kuti lisayende panjira yawo.+ 16 Chifukwa mapazi awo amathamangira zoipa,+ ndipo iwo amafulumira kukakhetsa magazi.+ 17 N’zopanda phindu kuyala ukonde pamaso pa chilichonse chokhala ndi mapiko.+ 18 Chotero anthu ochimwa amabisala kuti akhetse magazi a anthu ena.+ Amabisalira miyoyo ya anthu ena.+ 19 Umu ndi mmene zimakhalira njira za aliyense wopeza phindu mwachinyengo.+ Phindulo limachotsa moyo wa eni akewo.+
20 Nzeru yeniyeni+ imangokhalira kufuula mumsewu.+ Imangokhalira kutulutsa mawu ake m’mabwalo a mzinda.+ 21 Iyo imafuula kumapeto kwa misewu yaphokoso.+ Pazipata zolowera mumzinda, imanena mawu ake kuti:+
22 “Anthu osadziwa inu, kodi mukufuna kukhalabe osadziwa mpaka liti?+ Inu onyoza, mukufuna kukhalabe onyoza mpaka liti?+ Ndipo opusa inu, mudana ndi kudziwa zinthu mpaka liti?+ 23 Mverani kudzudzula kwanga ndipo mubwerere.+ Mukatero ndidzachititsa kuti mzimu wanga usefukire kwa inu+ ndipo ndidzakudziwitsani mawu anga.+ 24 Popeza ndaitana koma inu mukupitiriza kukana,+ ndatambasula dzanja langa koma palibe amene akumvetsera,+ 25 mukungonyalanyaza malangizo anga onse,+ ndipo simunamvere kudzudzula kwanga,+ 26 ineyo ndidzakusekani tsoka likadzakugwerani.+ Ndidzakunyozani zimene mumaopa zikadzabwera,+ 27 zimene mumaopa zikadzabwera ngati mvula yamkuntho, tsoka likadzakufikirani ngati mphepo yamkuntho,+ ndiponso masautso ndi nthawi zovuta zikadzakugwerani.+ 28 Pa nthawi imeneyo azidzangondiitana koma sindidzayankha.+ Adzakhalira kundifunafuna koma sadzandipeza,+ 29 chifukwa chakuti anadana ndi kudziwa zinthu+ ndipo sanasankhe kuopa Yehova.+ 30 Sanamvere malangizo anga.+ Sanalemekeze kudzudzula kwanga konse.+ 31 Chotero adzadya zipatso za njira yawo,+ ndipo adzakhuta malangizo awo.+ 32 Pakuti kupanduka+ kwa osadziwa n’kumene kudzawaphe+ ndipo mphwayi za opusa n’zimene zidzawawononge.+ 33 Koma munthu wondimvera adzakhala mwabata+ ndipo sadzasokonezeka chifukwa choopa tsoka.”+