17 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa milungu+ ndi Mbuye wa ambuye.+ Iye ndi Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa,+ amene sakondera+ munthu aliyense ndipo salandira chiphuphu.+
6 Tsopano kunena za anthu amene ankaoneka ngati apadera,+ kaya pa chiyambi anali anthu otani, zilibe kanthu kwa ine,+ Mulungu sayang’ana nkhope ya munthu,+ kwa ine, amuna odalirika amenewo sanandiphunzitse kalikonse katsopano.
9 Inu ambuye, muzichitiranso akapolo anu chimodzimodzi ndipo muleke kuwaopseza,+ pakuti mukudziwa kuti Ambuye wa nonsenu, wa iwowo ndi wa inuyo,+ ali kumwamba ndipo alibe tsankho.+