15 Abwanamkubwa amene analipo ine ndisanakhale, ankalemetsa anthu, ndipo tsiku ndi tsiku anali kulandira masekeli 40 a siliva kuti akagule chakudya ndi vinyo. Komanso atumiki awo anali kupondereza anthu.+ Koma ine sindinachite zimenezo+ chifukwa choopa Mulungu.+