Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Mbiri 28:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 “Ndipo iwe Solomo mwana wanga, dziwa+ Mulungu wa bambo wako, um’tumikire+ ndi mtima wathunthu+ ndi moyo wosangalala,+ chifukwa Yehova amasanthula mitima yonse+ ndipo amazindikira maganizo a munthu ndi zolinga zake zonse.+ Ukam’funafuna, adzalola kuti um’peze,+ koma ukam’siya+ adzakutaya kosatha.+

  • Salimo 62:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Komanso kukoma mtima kosatha ndi kwanu, inu Yehova,+

      Pakuti inu mumabwezera aliyense mogwirizana ndi ntchito zake.+

  • Miyambo 24:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Ukanena kuti: “Ifetu izi sitinali kuzidziwa,”+ kodi amene amafufuza mitima sazindikira zimenezo?+ Ndipo kodi amene amayang’anitsitsa moyo wako sadziwa zimenezo+ n’kubwezera munthu wochokera kufumbi mogwirizana ndi ntchito yake?+

  • Yeremiya 32:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Zolinga zanu ndi zazikulu+ ndipo zochita zanu ndi zambiri.+ Maso anu amaona njira zonse za ana a anthu+ kuti munthu aliyense mumuchitire zinthu mogwirizana ndi njira zake komanso zipatso za ntchito zake.+

  • Ezekieli 33:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 “Anthu inu mwanena kuti, ‘Njira za Yehova n’zopanda chilungamo.’+ Inu a nyumba ya Isiraeli, ine ndidzaweruza aliyense wa inu malinga ndi njira zake.”+

  • Mateyu 16:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Pakuti Mwana wa munthu adzabwera ndithu mu ulemerero wa Atate wake limodzi ndi angelo ake. Pa nthawi imeneyo adzapatsa aliyense mphoto malinga ndi makhalidwe ake.+

  • Aroma 2:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Iye adzaweruza aliyense malinga ndi ntchito zake motere:+

  • 2 Akorinto 5:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pakuti mtima wa aliyense wa ife udzaonekera pamaso pa mpando woweruzira milandu wa Khristu,+ kuti aliyense alandire mphoto yake pa zinthu zimene anachita ali m’thupi, mogwirizana ndi zimene anali kuchita, zabwino kapena zoipa.+

  • Agalatiya 6:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Musanyengedwe,+ Mulungu sapusitsika.+ Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.+

  • 1 Petulo 1:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Ndiponso, ngati mukupempha zinthu kwa Atate, amene amaweruza mopanda tsankho+ malinga ndi ntchito za aliyense, chitani zinthu ndi mantha+ pa nthawi imene muli ngati alendo m’dzikoli.+

  • Chivumbulutso 22:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “‘Taonani! Ndikubwera mofulumira,+ ndipo mphoto+ ndili nayo, yoti ndipereke kwa aliyense malinga ndi ntchito yake.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena