Genesis 6:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Pamenepo, Yehova anaona kuti kuipa kwa anthu kwachuluka padziko lapansi, ndipo malingaliro+ onse a m’mitima ya anthu anali oipa okhaokha nthawi zonse.+ Deuteronomo 31:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Ndiyeno masoka ndi zowawa zambiri zikadzawagwera,+ nyimboyi idzawayankha monga mboni, chifukwa siyenera kuchoka pakamwa pa mbadwa zawo, pakuti ndikudziwa mtima+ umene akuyamba kukhala nawo lero ndisanawalowetse m’dziko limene ndawalumbirira.” Salimo 139:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Inu mumadziwa ndikakhala pansi kapena ndikaimirira.+Mumadziwa maganizo anga muli kutali.+
5 Pamenepo, Yehova anaona kuti kuipa kwa anthu kwachuluka padziko lapansi, ndipo malingaliro+ onse a m’mitima ya anthu anali oipa okhaokha nthawi zonse.+
21 Ndiyeno masoka ndi zowawa zambiri zikadzawagwera,+ nyimboyi idzawayankha monga mboni, chifukwa siyenera kuchoka pakamwa pa mbadwa zawo, pakuti ndikudziwa mtima+ umene akuyamba kukhala nawo lero ndisanawalowetse m’dziko limene ndawalumbirira.”