Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 16:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Koma Yehova anauza Samueli kuti: “Usaone maonekedwe ake ndi kutalika kwa msinkhu wake,+ pakuti ine ndamukana ameneyu. Chifukwa mmene munthu amaonera si mmene Mulungu amaonera.+ Munthu amaona zooneka ndi maso,+ koma Yehova amaona mmene mtima ulili.”+

  • Yobu 34:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Pakuti iye amapereka mphoto kwa munthu wochokera kufumbi malinga ndi zochita zake,+

      Ndipo amam’bweretsera zinthu zogwirizana ndi njira yake.

  • Miyambo 24:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Ukanena kuti: “Ifetu izi sitinali kuzidziwa,”+ kodi amene amafufuza mitima sazindikira zimenezo?+ Ndipo kodi amene amayang’anitsitsa moyo wako sadziwa zimenezo+ n’kubwezera munthu wochokera kufumbi mogwirizana ndi ntchito yake?+

  • Yeremiya 32:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Zolinga zanu ndi zazikulu+ ndipo zochita zanu ndi zambiri.+ Maso anu amaona njira zonse za ana a anthu+ kuti munthu aliyense mumuchitire zinthu mogwirizana ndi njira zake komanso zipatso za ntchito zake.+

  • Ezekieli 7:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Mfumu idzalira,+ ndipo ngakhale mtsogoleri adzagwidwa ndi mantha.+ Manja a anthu a m’dzikolo adzanjenjemera chifukwa cha chisokonezo. Ndidzawachitira zinthu zogwirizana ndi njira zawo.+ Ndidzawaweruza mogwirizana ndi ziweruzo zawo.+ Chotero iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”+

  • Aroma 2:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Iye adzaweruza aliyense malinga ndi ntchito zake motere:+

  • 2 Akorinto 5:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pakuti mtima wa aliyense wa ife udzaonekera pamaso pa mpando woweruzira milandu wa Khristu,+ kuti aliyense alandire mphoto yake pa zinthu zimene anachita ali m’thupi, mogwirizana ndi zimene anali kuchita, zabwino kapena zoipa.+

  • Agalatiya 6:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Musanyengedwe,+ Mulungu sapusitsika.+ Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.+

  • Akolose 3:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Ndithudi, amene akuchita zolakwa adzalandiranso+ zolakwa zake zimene akuchitazo, chifukwa Mulungu sakondera.+

  • 2 Timoteyo 4:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Alekizanda,+ wosula zinthu zamkuwa uja, anandichitira zoipa zambiri. Yehova adzamubwezera malinga ndi ntchito zake,+

  • 1 Petulo 1:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Ndiponso, ngati mukupempha zinthu kwa Atate, amene amaweruza mopanda tsankho+ malinga ndi ntchito za aliyense, chitani zinthu ndi mantha+ pa nthawi imene muli ngati alendo m’dzikoli.+

  • Chivumbulutso 20:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Ndiye ndinaona akufa, olemekezeka ndi onyozeka,+ ataimirira pamaso pa mpando wachifumuwo, ndipo mipukutu inafunyululidwa. Koma mpukutu wina unafunyululidwa, ndiwo mpukutu wa moyo.+ Ndipo akufa anaweruzidwa malinga ndi zolembedwa m’mipukutuyo, mogwirizana ndi ntchito zawo.+

  • Chivumbulutso 22:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “‘Taonani! Ndikubwera mofulumira,+ ndipo mphoto+ ndili nayo, yoti ndipereke kwa aliyense malinga ndi ntchito yake.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena