Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Mafumu 8:39
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 39 inuyo mumve muli kumwamba,+ malo anu okhala okhazikika+ ndipo mukhululuke+ ndi kuchitapo kanthu.+ Mupatse aliyense malinga ndi njira zake zonse,+ popeza mukudziwa mtima wake+ (popeza inuyo nokha mumadziwa bwino mtima wa ana onse a anthu).+

  • 1 Mbiri 28:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 “Ndipo iwe Solomo mwana wanga, dziwa+ Mulungu wa bambo wako, um’tumikire+ ndi mtima wathunthu+ ndi moyo wosangalala,+ chifukwa Yehova amasanthula mitima yonse+ ndipo amazindikira maganizo a munthu ndi zolinga zake zonse.+ Ukam’funafuna, adzalola kuti um’peze,+ koma ukam’siya+ adzakutaya kosatha.+

  • 2 Mbiri 16:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Pajatu maso a Yehova+ akuyendayenda padziko lonse lapansi+ kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo+ uli wathunthu kwa iye. Mwachita zopusa+ pankhani imeneyi, chifukwa kuyambira tsopano anthu azichita nanu nkhondo.”+

  • Salimo 7:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Chonde, thetsani kuipa kwa anthu oipa,+

      Ndipo khazikitsani wolungama.+

      Mulungu pokhala wolungama+ akuyesa mtima+ ndi impso.+

  • Miyambo 24:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Ukanena kuti: “Ifetu izi sitinali kuzidziwa,”+ kodi amene amafufuza mitima sazindikira zimenezo?+ Ndipo kodi amene amayang’anitsitsa moyo wako sadziwa zimenezo+ n’kubwezera munthu wochokera kufumbi mogwirizana ndi ntchito yake?+

  • Yeremiya 17:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ine Yehova ndimafufuza mtima+ ndi kusanthula impso.+ Munthu aliyense ndimamuchitira zinthu monga mwa zochita zake,+ mogwirizana ndi zipatso za ntchito zake.+

  • Machitidwe 1:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Ndipo anapemphera kuti: “Ambuye wathu Yehova, inu amene mumadziwa mitima ya anthu onse,+ tisonyezeni amene inu mwamusankha mwa amuna awiriwa,

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena