20 Koma Yehova wa makamu amaweruza mwachilungamo.+ Amafufuza impso ndi mtima.+ Inu Mulungu, ndiloleni ndione mukuwapatsa chilango, pakuti ine ndakufotokozerani mlandu wanga.+
10 Ine Yehova ndimafufuza mtima+ ndi kusanthula impso.+ Munthu aliyense ndimamuchitira zinthu monga mwa zochita zake,+ mogwirizana ndi zipatso za ntchito zake.+
23 Ana ake ndidzawapha ndi mliri wakupha, moti mipingo yonse idzadziwa kuti ineyo ndiye amene ndimafufuza impso ndi mitima, ndipo ndidzabwezera mmodzi ndi mmodzi wa inu malinga ndi ntchito zake.+