Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 16:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Koma Yehova anauza Samueli kuti: “Usaone maonekedwe ake ndi kutalika kwa msinkhu wake,+ pakuti ine ndamukana ameneyu. Chifukwa mmene munthu amaonera si mmene Mulungu amaonera.+ Munthu amaona zooneka ndi maso,+ koma Yehova amaona mmene mtima ulili.”+

  • 1 Mbiri 28:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 “Ndipo iwe Solomo mwana wanga, dziwa+ Mulungu wa bambo wako, um’tumikire+ ndi mtima wathunthu+ ndi moyo wosangalala,+ chifukwa Yehova amasanthula mitima yonse+ ndipo amazindikira maganizo a munthu ndi zolinga zake zonse.+ Ukam’funafuna, adzalola kuti um’peze,+ koma ukam’siya+ adzakutaya kosatha.+

  • Salimo 7:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Chonde, thetsani kuipa kwa anthu oipa,+

      Ndipo khazikitsani wolungama.+

      Mulungu pokhala wolungama+ akuyesa mtima+ ndi impso.+

  • Miyambo 11:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Anthu a mtima wopotoka amam’nyansa Yehova,+ koma anthu opanda cholakwa m’njira yawo amam’sangalatsa.+

  • Yeremiya 17:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ine Yehova ndimafufuza mtima+ ndi kusanthula impso.+ Munthu aliyense ndimamuchitira zinthu monga mwa zochita zake,+ mogwirizana ndi zipatso za ntchito zake.+

  • Yeremiya 20:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Inu Yehova wa makamu, mumasanthula munthu wolungama.+ Mumaona impso ndi mtima wake.+ Ndiloleni ndione mukuwapatsa chilango,+ pakuti ine ndakufotokozerani mlandu wanga.+

  • Chivumbulutso 2:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Ana ake ndidzawapha ndi mliri wakupha, moti mipingo yonse idzadziwa kuti ineyo ndiye amene ndimafufuza impso ndi mitima, ndipo ndidzabwezera mmodzi ndi mmodzi wa inu malinga ndi ntchito zake.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena