Yobu
35 Elihu anapitiriza kulankhula kuti:
2 “Kodi mukuona ngati chimenechi n’chilungamo?
Inuyo mwanena kuti, ‘Ndine wolungama kuposa Mulungu.’+
3 Mwanena kuti, ‘Kodi kulungamako n’kwantchito yanji kwa inu?+
Kodi kundipindulitsa chiyani kuposa chimene ndikanapindula pochimwa?’+
6 Mukachimwa, kodi mumapindula chiyani chotsutsana naye?+
Ndipo kupanduka kwanu kukawonjezeka, kodi mumam’chitira chiyani chomuipira?
7 Ngati ndinudi wosalakwa, kodi mumam’patsa chiyani?
Kodi amalandira chiyani kuchokera m’manja mwanu?+
8 Kuipa kwanu kungapweteke munthu ngati inu nomwe,+
Ndipo chilungamo chanu chingakomere mwana wa munthu wochokera kufumbi.+
9 Chifukwa cha kuchuluka kwa kuponderezedwa, iwo amangokhalira kufuula popempha thandizo.+
Amangokhalira kulirira thandizo chifukwa cha dzanja la amphamvu.+
10 Koma palibe wanena kuti, ‘Kodi Mulungu, Wondipanga Wamkulu,+ ali kuti,
Amene amapatsa anthu nyimbo usiku?’+
11 Iye ndiye amatiphunzitsa+ zambiri kuposa nyama zakutchire,+
Ndipo amatipatsa nzeru kuposa ngakhale zolengedwa zouluka m’mlengalenga.