Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g03 12/8 tsamba 25-26
  • Mmene Dziko Lapansili Lidzapulu Mutsidwire

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Dziko Lapansili Lidzapulu Mutsidwire
  • Galamukani!—2003
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Njira Yabwino Yothetsera Mavutoŵa Yayandikira
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kusamalira Chilengedwe?
    Galamukani!—2007
  • Moyo Uli ndi Chifuno Chachikulu
    Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
  • Kodi Ndi Ndani Amene Adzapulumutse Dzikoli?
    Nkhani Zina
  • Kodi Dzikoli Lidzatha?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Galamukani!—2003
g03 12/8 tsamba 25-26

Mmene Dziko Lapansili Lidzapulu Mutsidwire

NGAKHALE kuti dziko lapansi likuwonongedwa kwambiri, tikufuna kuti lidzapulumuke. Izi zili choncho chifukwa dziko lapansili ndiye kwathu, ndipo tili ndi chiyembekezo choti lidzakhalanso kwawo kwa ana athu ndi ana awo. Kodi pali chilichonse chimene tingachite kuti zimenezi zidzachitikedi?

N’zoona kuti anthu ambiri amada nkhaŵa ndi chilengedwe, koma ambiri saganiza kuti n’kulakwa kutaya zinyalala pansi, mu mtsinje, kapena kusiya magetsi ali oyaka pamene sakuwagwiritsa ntchito. Zinthu zimenezi zingawoneke ngati zochepa, koma ngati munthu aliyense pa anthu mabiliyoni ambiri amene ali padziko lapansi akanati azisamalira dzikoli, zinthu zikanatha kusintha. Zinthu ngati kusamala pogwiritsa ntchito magetsi, ndi kutaya zinyalala moyenera zimathandiza poteteza chilengedwe. Mwa zimene timachita pakadali pano tingasonyeze kuti timasamalira dziko lapansili.

Komabe, sitingathe kulamulira zochita za anthu ena amene timakhala nawo pafupi. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti sizidzatheka kuti dziko litetezedwe?

Njira Yabwino Yothetsera Mavutoŵa Yayandikira

Mawu amene Thilo Bode wa m’bungwe la Greenpeace ananena m’magazini ya Time akufotokoza vuto lenileni limene limachititsa mavuto a zachilengedwe. Iye anati: “Cholinga chathu chachikulu n’choti mabungwe aziganizira mmene zinthu zawo zimatayidwira zikatha ntchito. Mabungwewo ayenera kuganizira zinthu zitatu: kupanga zinthu, kuzigwiritsa ntchito, ndiponso kuzitaya kwake.” Chomvetsa chisoni n’chakuti timatha kupanga zinthu, timadziŵa kuzigwiritsa ntchito, koma sitizitaya moyenera tikatha kuzigwiritsa ntchito. Nthaŵi zina anthu sadziŵa n’komwe mmene angatayire zinthu moyenera.

Nzeru za anthu n’zopereŵera, koma za Mlengi wa dziko lapansi sizopereŵera. Mlengi wasonyeza kale nzeru zake zapamwamba m’zinthu zimene analenga zimene timaziona padziko lapansi. Amadziŵa kupanga, kugwiritsa ntchito, ndi kutaya zinthu moyenera zikatha ntchito. Zinthu zambiri zimene analenga zimadzikonza zokha. Njere imamera, ndipo ikamera mtengo wakewo umakula n’kubala chipatso. Kenaka mtengowo umafa, ndipo zinthu zonse zimene zinali mu mtengomo zimawola popanda kuipitsa chinthu chilichonse, kenaka zimagwiritsidwanso ntchito. Kumeneku n’kutaya zinyalala kwabwinodi kwambiri! Sikutulutsa poizoni wowononga!

Mlengi sakufuna kuti dziko lapansili lisanduke dzala lazinyalala loti anthu sangakhalemonso. M’Baibulo, pa Yesaya 45:18 timaŵerenga kuti: “Atero Yehova . . . Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu.”

Ngati Mulungu analenga dziko lapansi kuti anthu akhalemo, n’chifukwa chiyani walola kuti lifike poipa ngati pamene lafikapa? Baibulo limafotokoza kuti munthu poyambirira anamuika m’paradaiso. Ndipo Mulungu anafuna kuti Paradaiso ameneyu afalikire padziko lonse lapansi ndipo anthu adzazemo. (Genesis 1:28) Komabe, anthu anapanduka. Mwamuna ndi mkazi woyamba sanafune kupitiriza kugonjera ulamuliro wa Mulungu.

Mulungu analola anthu kuyesera kudzilamulira okha. Zotsatira zake n’zimene tikuziona lerozi. Anthu alephera momvetsa chisoni. Asonyeza poyera kuti sangathe kuthetsa mavuto awo. Sitinganene kuti zimene zachitikazi wachititsa ndi Mulungu. Zimene Baibulo limanena zikukhudza anthu onse. Ilo limati: “Anam’chitira zovunda si ndiwo ana ake, chilema n’chawo; iwo ndiwo mbadwo wopulukira ndi wokhotakhota.”—Deuteronomo 32:5.

Komabe, sikuti kuwonongeka kwa dzikoli sikukumukhudza Mulungu. Adzachitapo kanthu pa nthaŵi yake, dziko lapansili lisanasanduke malo oipa oti anthu sangakhaleponso. Kodi tikudziŵa bwanji zimenezi? Lemba la Chivumbulutso 11:18 limafotokoza kuti: “Amitundu anakwiya, ndipo unadza mkwiyo wanu, ndi nthaŵi ya . . . kuwononga iwo akuwononga dziko.” Kuwononga dziko lapansi kudzathetsedwa.

Cholinga choyambirira cha Mulungu polenga dziko lapansi, choti likhale paradaiso, chidzakwaniritsidwa. Mulungu ananena mawu osonyeza zimenezi. Mwachitsanzo, iye anati: “Mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna.” (Yesaya 55:11) Mungasangalale mutaŵerenga Yesaya chaputala 35, pamene Mulungu akufotokoza za kusintha kwa malo owonongeka kusanduka minda yokongola yodzala ndi zipatso.

Ngakhale panopa, kumalo kumene anthu anasiya kuwononga malo, dziko lapansi lasonyeza kuti lili ndi mphamvu zodabwitsa zotha kudzikonza lokha. Mulungu analilenga kuti lizitero. Kuwononga dziko kutalekeka, tizilombo tosaoneka ndi maso tosiyanasiyana tam’madzi ndi m’dothi tikhoza kubwezeretsa m’chimake zinthu zambiri zimene zawonongeka padzikoli. Kuwonjezera apo, tili ndi zifukwa zokhulupirira kuti Mulungu akadzaloŵererapo n’kuyamba kuyendetsa zinthu, kubwezeretsa kumeneku kudzayenda bwino kwambiri kuposa mmene kungachitire panopa. Mulungu angaphunzitse ndi kutsogolera anthu bwino kwambiri, zinthu zimene anthu panopa sangathe.

Choncho, si kuti dziko lapansi silidzakhala ndi tsogolo labwino. Zomera ndi nyama zidzapulumuka. Sikudzakhalanso nyama ndi zomera zimene zidzatsale pang’ono kutha. Madzi ndi mpweya wathu zidzakhalanso zabwino. Anthu omvera adzasangalala nazo zimenezi. Kodi mungakonde kuona zimenezi zikuchitika? Mukhoza kutero. Motani? Baibulo limafotokoza zimene muyenera kuchita. Bwanji osafufuza Baibulo mwatsatanetsatane kuti mudziŵe zimenezi panokha? Funsani ofalitsa magazini ino kuti akuthandizeni kukumana ndi munthu amene angakuthandizeni kuyamba kuchita zimenezi. Musaphonye mwayi wophunzira mmene inuyo ndi banja lanu mungadzakhalire osangalala m’malo okongola mpaka kalekale.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena