Panagona Luso!
Kuwala kwa Ziphaniphani
● M’madera otentha a padziko lapansi, mumapezeka tizilombo totchedwa ziphaniphani. Tizilomboti timawala ngati magetsi tikafuna kukopa tizilombo tatimuna kapena tatikazi. Kuwala kwa ziphaniphani kumaposa kuwala kwa mababu wamba kapena kwa mababu owala kwambiri amene anthu amapanga, chifukwa tizilomboti tikamawala sititentha. Choncho, nthawi ina mukamadzalandira bilu yanu ya magetsi, mudzaganizire za tizilombo timeneti.
Taganizirani izi: Pa mphamvu yonse imene mababu wamba amatulutsa, 10 peresenti ndi imene imasinthidwa kukhala kuwala ndipo 90 peresenti yotsalayo imangowonongeka. Mababu owala kwambiri amachitako bwino chifukwa mphamvu imene imasinthidwa kukhala kuwala ndi 90 peresenti ndipo 10 peresenti yokha ndi imene imawonongeka. Mphamvu yowonongekayo ndi imene imachititsa kuti mababuwo azitentha. Koma mitundu iwiri ya mababuyi imaposedwa ndi ziphaniphani. Pafupifupi mphamvu yonse imene tizilombo timeneti timatulutsa imasinthidwa kukhala kuwala ndipo mphamvu imene imawonongeka ndi yochepa kwambiri.
Chinsinsi cha ziphaniphani chagona pa kemiko inayake. Kemiko imeneyi ikaphatikizana ndi okosijeni mothandizidwa ndi kemiko inanso, kachilomboka kamayamba kuwala. Mosiyana ndi mababu amene akamawala amatentha, tizilomboti sititentha, timangowala basi. Mlangizi wina wa kalimidwe ka mbewu ndiponso kasamalidwe ka zinthu zachilengedwe, dzina lake Sandra Mason, anafotokoza kuti Thomas Edison, yemwe anali munthu woyamba kupanga mababu a magetsi, “ayenera kuti ankachita nsanje akaona kuwala kwa ziphaniphani.”
Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika mwangozi kuti ziphaniphani zizitulutsa kuwala kotereku, kapena pali Mlengi amene anazipanga?
[Zithunzi patsamba 15]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
MPHAMVU ZIMENE ZIMASINTHIDWA N’KUKHALA KUWALA
10 peresenti 90 peresenti 96 peresenti
Babu wamba Babu lowala kwambiri Chiphaniphani
[Mawu a Chithunzi patsamba 15]
Firefly on leaf: © E. R. Degginger/Photo Researchers, Inc.; firefly in flight: © Darwin Dale/Photo Researchers, Inc.