Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 9/10 tsamba 21-31
  • Zoti Banja Likambirane

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zoti Banja Likambirane
  • Galamukani!—2010
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Anaganiza Bwino?
  • KODI MUKUDZIWA CHIYANI ZOKHUDZA MTUMWI YOHANE?
  • ZITHUNZI ZOTI ANA APEZE
  • KUCHOKERA M’MAGAZINI INO
  • MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31
  • Zoti Banja Likambirane
    Galamukani!—2010
  • Zoti Banja Likambirane
    Galamukani!—2010
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
    Galamukani!—2008
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
    Galamukani!—2008
Onani Zambiri
Galamukani!—2010
g 9/10 tsamba 21-31

Zoti Banja Likambirane

Kodi Anaganiza Bwino?

Werengani Maliko 12:41-44. Kenako onani chithunzichi ndipo lembani mayankho anu m’mizere ili m’munsiyi.

1. Kodi zinthu zoponyamo zopereka zinkakhala kuti?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Maliko 12:35; 13:1.

․․․․․

2. Ngakhale kuti mkazi wamasiye anapereka ndalama zochepa, n’chifukwa chiyani Yesu anamuyamikira?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Maliko 12:28-30.

․․․․․

3. Kodi n’chifukwa chiyani munganene motsimikiza kuti mkazi wamasiyeyo sanavutike ataponya ndalama “zonse zimene anali nazo”?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Mateyo 6:25, 31-33.

․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi mukuganiza kuti mkazi wamasiyeyo anaganiza bwino? N’chifukwa chiyani mukuyankha choncho? Kodi ubwino wokhala ndi chizolowezi chopereka mowolowa manja ndi wotani?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Luka 6:38; Machitidwe 20:35.

KODI MUKUDZIWA CHIYANI ZOKHUDZA MTUMWI YOHANE?

4. Kodi atsogoleri achipembedzo ankaona kuti Yohane ndi wophunzira?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Machitidwe 4:13.

․․․․․

5. Kodi Yohane anapatsidwa mwayi wochita chiyani?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Chivumbulutso 1:1-3.

․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi Yohane analemba mabuku angati? Kodi mungatsanzire bwanji Yohane?

ZITHUNZI ZOTI ANA APEZE

Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Kenako fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

KUCHOKERA M’MAGAZINI INO

Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.

TSAMBA 9 Kodi n’chiyani chimabweretsa chisangalalo chochuluka? Machitidwe 20:․․․

TSAMBA 9 Kodi ophunzira a Yesu tingawazindikire bwanji? Yohane 13:․․․

TSAMBA 21 Kodi mtendere wa Mulungu ungathe kuchita chiyani? Afilipi 4:․․․

TSAMBA 22 Kodi Yehova amakhala pafupi ndi ndani? Salmo 34:․․․

● Mayankho ali patsamba 21

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31

1. M’kachisi.

2. Chifukwa anapereka kwa Mulungu zonse zimene akanatha kupereka.

3. Mulungu analonjeza kuti adzatisamalira ngati tikuika zinthu zake patsogolo.

4. Ayi. Iwo ankaona kuti Yohane ndi munthu wamba komanso wosaphunzira.

5. Anauziridwa kulemba mabuku ena a m’Baibulo, kuphatikizapo Chivumbulutso.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena