Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 1/11 tsamba 32
  • “Ndinalira Nditaliwerenga”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Ndinalira Nditaliwerenga”
  • Galamukani!—2011
Galamukani!—2011
g 1/11 tsamba 32

“Ndinalira Nditaliwerenga”

● Zimenezi n’zimene ananena mayi wina, yemwe amakhala ku Illinois, m’dziko la America., atawerenga buku lakuti Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Iye analembera kalata ofalitsa a bukuli, ndipo m’kalatamo anati, “Ndikulakalaka ndiponso kupemphera kuti anthu ambiri awerenge bukuli n’kusangalala ndi nkhani za Yesu ngati mmene ineyo ndachitira.”

Buku la Munthu Wamkulu limafotokoza za moyo wa Yesu potengera mabuku ouziridwa a Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane. Anthu amenewa anakhala ndi moyo m’nthawi ya Yesu. Mateyu ndi Yohane anali atumwi a Yesu ndipo ankayenda naye limodzi. Maliko anali mnzake wapamtima wa Petulo, yemwe anali mtumwi wa Yesu. Ndipo Luka, yemwe anali dokotala, anali mnzake wa Paulo amene ankayenda naye.

Ngati mungafune kupatsidwa buku lokhala ndi zithunzi zokongola limeneli, lembani zofunika m’munsimu ndipo tumizani ku adiresi yoyenera pa maadiresi amene ali patsamba 5 m’magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire bukuli.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena