Zoti Banja Likambirane
Kodi Chithunzichi Chalakwika Pati?
Werengani Yohane 6:5-13. Tchulani zinthu zitatu zomwe zalakwika pachithunzichi. Lembani mayankho anu m’munsimu. Ndipo malizitsani kujambula chithunzichi pochichekenira.
1. ․․․․․
2. ․․․․․
3. ․․․․․
KAMBIRANANI:
Kodi Yesu anauza ophunzira ake kuti asonkhanitse chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani? Kodi zimenezi zikukuphunzitsani chiyani zokhudza Yesu? Kodi mungatani kuti musamawononge zakudya kapena zinthu zina?
ZOTI BANJA LICHITIRE PAMODZI:
Werengani nkhaniyo pamodzi m’Baibulo. Ngati n’kotheka, sankhani munthu mmodzi kuti akhale munthu wofotokoza nkhaniyo, wina akhale Yesu, wina Filipi ndipo wina akhale Andireya.
Sungani Kuti Muzikumbukira
Dulani, pindani pakati n’kusunga
KHADI LA BAIBULO 1 YOSWA
MAFUNSO
A. Kodi Yoswa ndi asilikali ake anatani kuti athe kugwetsa makoma a Yeriko?
B. Malizitsani mawu a Yoswa awa: “Ine ndi a m’nyumba yanga . . . ”
C. Kodi Yoswa ankadziwikanso ndi mayina ena ati?
[Tchati]
4026 B.C.E. 1 C.E. 98 C.E.
Kulengedwa kwa Adamu Anakhala ndi moyo Baibulo linamalizidwa
cha m’ma 1500’s B.C.E. kulemba
[Mapu]
Anachoka ku Iguputo kupita ku Dziko Lolonjezedwa
IGUPUTO
DZIKO LOLONJEZEDWA
YOSWA
ANALI NDANI?
Mwana wa Nuni. Anali mtumiki wa Mose, kenako anasankhidwa kuti atsogolere mtundu wa Isiraeli. (Ekisodo 33:11; Deuteronomo 34:9; Yoswa 1:1, 2) Yoswa anatsogolera anthu a Mulungu molimba mtima popita ku Dziko Lolonjezedwa. Ankakhulupirira malonjezo a Yehova, ankamvera malangizo ake, ndipo ankamutumikira mokhulupirika.
MAYANKHO
A. Anamvera Mulungu poguba kuzungulira mzindawo.—Yoswa 6:1-27.
B. “. . . tizitumikira Yehova.”—Yoswa 24:15.
C. Hoshiya ndi Yehoswa.—Numeri 13:8, 16.
Anthu ndi Mayiko
4. Dzina langa ndi Victor. Ndili ndi zaka 7 ndipo ndimakhala ku Malawi. Dzikoli limapezeka ku Africa. Kodi mukudziwa kuti ku Malawi kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko pafupifupi 750, 7,500, kapena 75,000?
5. Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene ndimakhala? Jambulani mzere wozungulira kadonthoko, ndipo kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi la Malawi.
A
B
C
D
Zithunzi Zoti Ana Apeze
Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.
● Mayankho a mafunso a patsamba 30 ndi 31 ali patsamba 22.
MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 30 ndi 31
1. Wagwira mbale ya zakudyayo ayenera kukhala mnyamata, osati mtsikana.
2. M’mbalemo muyenera kukhala buledi musanu, osati maapozi asanu.
3. Muyenera kukhala nsomba ziwiri, osati chimanga chiwiri.
4. 75,000.
5. C.