Ndinali Munthu Woopsa Kwambiri
Yosimbidwa ndi Jose Antonio Nebrera
KODI n’chiyani chimachititsa munthu kukhala wankhanza? Ineyo ndinaphunzira moyo wankhanza kuchokera kwa makolo anga, omwe ankandizunza kwambiri ndili mwana. Bambo anga anali m’gulu la asilikali ankhanza kwambiri ku Spain. Iwo ali mwana, bambo awo ankakonda kuwamenya kwambiri, ndipo nawonso anatengera zomwezo. Nthawi zambiri ankandikwapula pogwiritsa ntchito lamba wokhuthala kwambiri. Kuwonjezera pamenepa, ankakonda kunena kuti ndine chitsiru, pamene mchemwali wanga wamng’ono ankamukonda kwambiri. Mayi anga ankawaopa kwambiri bambo, choncho sankanditeteza kapena kundisonyeza chikondi chimene ndinkachisowa kwambiri.
Ndikapita kusukulu, ndinkasonyeza anzanga kuti zinthu zili bwinobwino pa moyo wanga. Ndipo anzanga ena ankaona ngati ndine wosangalala. Koma zonsezi zinali zonamizira. Sindinkafuna kuti anthu adziwe kuti mumtima mwanga mwadzaza mkwiyo komanso mantha. Koma ndinkati ndikaweruka n’kuyamba ulendo wobwerera kunyumba, ndinkachita mantha chifukwa ndinkadziwa kuti ndikafikira kukalipiridwa kapena kumenyedwa.
Ndili ndi zaka 13, ndinayamba sukulu yogonera komweko ya Akatolika n’cholinga choti ndithawe nkhanza zimene ndinkachitidwa kunyumba. Kwa nthawi ndithu, ndinkaganiza zodzakhala wansembe. Koma zimene zinkachitika kusukuluyi sizinandithandize kuti ndikhale ndi cholinga chenicheni pa moyo. Tsiku lililonse tinkadzuka 5 koloko m’mawa n’kukasamba madzi ozizira. Tikatero tinkapanikizika tsiku lonse ndi kuphunzira, kupemphera, ndi kuchita miyambo ina ya tchalitchi, ndipo tinkakhala ndi nthawi yochepa kwambiri yopuma.
Ngakhale kuti kusukuluko tinkafunika kuwerenga nkhani za “oyera mtima,” sitinkagwiritsa ntchito Baibulo. Baibulo limodzi lokha limene linalipo ankalitsekera mu bokosi lagalasi ndipo tinkafunikira kupempha chilolezo tikafuna kuliwerenga.
Titalowa chaka chachitatu cha maphunzirowa, tinayamba kuchita mwambo wodzimenyamenya. Nthawi zonse tinkachita zimenezi ndipo zinkandipweteka kwambiri. Pofuna kuzemba mwambowu, ndinkameza chakudya chambirimbiri osatafuna kuti ndidwale. Koma zimenezi sizinandithandize. Nditatha zaka zitatu ndili kusukuluyi, ndinakanika kupilira. Choncho, ndinathawa n’kupita kunyumba. Apa n’kuti ndili ndi zaka 16.
Ndinkafuna Kuchita Zinthu Zatsopano Nthawi Zonse
Ndili kunyumba, ndinayamba kuchita masewera a nkhonya komanso masewera ogwetsana pansi. Nthawi zambiri ndinkapambana pa masewera amenewa ndipo zimenezi zinkandipangitsa kumva kuti ndine munthu wofunika. Koma mphamvu zimenezi ndinkazigwiritsa ntchito molakwika chifukwa nthawi zina ndinkachitira anthu ena nkhanza n’cholinga choti zanga zindiyendere, ngati mmene ankachitira bambo anga.
Koma ndili ndi zaka 19, panachitika chinthu china chimene chinachititsa kuti mtima wanga ufewereko pang’ono. Ndinadziwana ndi Encarnita ndipo patapita miyezi 9 tili pachibwenzi, tinakwatirana. Iye ankangoona kuti ndine munthu wabwino, wachifundo ndiponso wosangalala. Koma sankadziwa kuti mumtima mwanga ndinkaganiza zinthu zankhanza chifukwa cha mmene ndinakulira. Nkhanza zimenezi zinadzaonekera nditaitanidwa kuti ndikalowe usilikali. Apa n’kuti mwana wathu woyamba atangobadwa kumene.
Koma popeza kuti ndinkafuna kuchita zinthu zatsopano nthawi zonse komanso sindinkafuna kuti ndizimeta tsitsi ngati msilikali, ndinadzipereka msangamsanga kuti ndizigwira ntchito m’gulu la asilikali a ku Spain amene ankatumizidwa m’mayiko ena. Ndinkaganiza kuti ndikapita kuchipululu cha ku Morocco n’kumakagwira ntchito zosiyanasiyana zoopsa kwambiri, ndikhala wosangalala. Komanso ndinkaona kuti zimenezi zindithandiza kuthawa udindo wosamalira banja langa. Koma pamapeto pake ndinakhala munthu woopsa kwambiri.
Pasanapite nthawi yaitali, ndinadziika m’mavuto. Mkulu wa asilikali amene ankatiyang’anira ankakonda kuzunza asilikali amene angoyamba kumene ntchito. Munthu akamachita zinthu zopanda chilungamo ndinkadana naye kwambiri ndipo sindinkaopa kumenyana naye. Tsiku lina m’mawa mkulu wa asilikaliyo akuitana mayina, ndinanena nthabwala imene iye anaimva molakwika. Iye anapsa mtima ndipo atanyamula dzanja lake kuti andimenye, ndinagwira mkono wake mwamsanga n’kuupotokola ndipo ndinamugwetsera pansi. Ndinamugwira moti asathenso kudzuka chifukwa ndikanangomusiya, akanandiwombera ndi mfuti yake yam’manja.
Zimenezi zinachititsa kuti nditsekeredwe m’ndende ya asilikali kwa miyezi itatu. Ananditsekera m’kachipinda kakang’ono, momwe ndinkakhalamo ndi akaidi enanso okwana 30. Pa nthawi yonseyi sankandilola kusintha ngakhale zovala zanga. Munthu amene ankatiyang’anira m’ndendemo anali wankhanza kwambiri ndipo ankakonda kukwapula akaidi. Pa nthawi ina ndinamuwopseza kuti akangondigwira ndimupha, choncho anandichepetsera chilango changa kuchoka pa zikwapu 30 kufika pa zikwapu zitatu. Ndinaphunzira kukhala wovuta kwambiri ngati anthu amene ankatizunzawo.
Ndinkagwira Ntchito Zoopsa Zachinsinsi
Pa nthawi yomwe ndinkachita maphunziro m’gulu la asilikali omwe ankafunika kutumizidwa kunja kwa dziko la Spain, ndinadzipereka msangamsanga kuti ndikagwire nawo ntchito inanso yoopsa kwambiri. Ulendo unonso sindinkadziwa bwinobwino kuti zimenezi zindifikitsa pati. Ndinaphunzitsidwa kugwiritsa ntchito mfuti za mtundu uliwonse komanso kutchera mabomba osiyanasiyana. Kenako ndinatumizidwa ku Langley, mumzinda wa Virginia, m’dziko la United States, kuti ndikamalize maphunziro anga. Kumeneko ndinaphunzitsidwa ndi akazitape a bungwe la CIA.
Pasanapite nthawi yaitali, ndinaikidwa m’gulu lachinsinsi logwira zigawenga. M’zaka za m’ma 1960, ndinagwira nawo ntchito zambirimbiri zachinsinsi. Ndinathandiza nawo kugwira anthu ozembetsa mankhwala osokoneza bongo komanso ozembetsa zida za nkhondo ku Central ndi South America. Tinkauzidwa kuti tikagwira anthu amenewa tiziwapha. Anthu amene tinkawasiya amoyo ndi amene tinkafuna kukawafunsa mafunso. Panopo ndimamva chisoni kwambiri kuti ndinapha nawo anthu amenewa.
Kenako ndinapatsidwa ntchito yomafufuza akuluakulu a asilikali a dziko la Spain kuti tipeze amene sankagwirizana ndi ulamuliro wa General Franco. Tinakafufuzanso ku France kuti tipeze anthu amene ankadana ndi ulamuliro wa Franco. Cholinga chathu chinali chakuti tigwire atsogoleri awo n’kupita nawo ku Spain kukawapha.
Chinthu choopsa komanso chomaliza chimene ndinachita chinali kusonkhanitsa asilikali aganyu oti akagwetse boma m’dziko linalake laling’ono ku Africa. Tinapatsidwa malangizo akuti tikawombere malo a asilikali ku likulu la dzikolo ndipo tikatero tikalande nyumba ya pulezidenti. Zinthu zinayendadi monga mmene tinakonzera. Tinalowa m’dzikolo pakati pa usiku ndipo tinamaliza ntchito yathu patangopita maola anayi okha. Pa kumenyanako, asilikali atatu okha a gulu lathu anafa, pamene ifeyo tinapha adani ambirimbiri. Ndimamvanso chisoni kuti ndinapha nawo anthu amenewa.
Zinthu zankhanza zimenezi zinkandivutitsa kwambiri maganizo. Ndinkalephera kugona chifukwa nthawi zonse ndikagona ndinkalota zinthu zoopsa. Ndinkalota ndikugwira adani n’kumawapha. M’malotowo, ndinkaona nkhope zomvetsa chisoni za anthu amene ndatsala pang’ono kuwapha.
Chifukwa cha zimenezi, ndinalumbira kuti nditauzidwanso kuti ndipite kwinakwake kukagwira ntchito yopha anthu, sindingapite. Choncho, ndinapereka zikalata zanga zonse za usilikali kwa akuluakulu n’kusiya ntchito. Komabe, patangopita miyezi itatu ndinaitanidwanso kuti ndikachite ntchito yoopsa ya ukazitape. Ndinathawira ku Switzerland ndipo patapita miyezi ingapo mkazi wanga ananditsatira kumene ndinkakhala ku Basel. Iye sankadziwa ngakhale pang’ono kuti ndinkagwira ntchito ya ukazitape.
Wachake Ndi Wachake
Pa zaka zitatu zimene ndinkagwira ntchito ya usilikali, mkazi wanga Encarnita anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ku Spain. Iye anandiuza kuti wapeza choonadi chokhudza Mulungu ndipo poona mmene ankasangalalira nanenso ndinali ndi chidwi choti ndiphunzire Baibulo. Mwamsanga tinafunafuna a Mboni za Yehova ku Switzerland ndipo titawapeza ine ndi mkazi wanga tinayamba kuphunzira Baibulo.
Ndinkasangalala kwambiri kuphunzira zinthu zosiyanasiyana zokhudza Mulungu ndi cholinga chake. Ndinkafunitsitsa kusintha moyo wanga n’kuyamba kutsatira mfundo za m’Baibulo, koma popeza amati wachake ndi wachake, ndinkavutika kwambiri kusiya moyo wanga wankhanza. Komabe, ndinkakonda kwambiri zinthu zimene ndinkaphunzirazo. Nditaphunzira kwa miyezi ingapo ndinaumirira kuti ndizigwira nawo ntchito ya Mboni za Yehova yolalikira kunyumba ndi nyumba.
Komabe Yehova anandithandiza ndipo pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kuchita zinthu moleza mtima. Patapita nthawi, ine ndi mkazi wanga tinabatizidwa. Ndili ndi zaka 29, ndinaikidwa kukhala woyang’anira mumpingo.
Mu 1975 tinaganiza zobwerera ku Spain. Koma akuluakulu a asilikali aja anali asanandiiwale ndipo anandiitana kuti ndikagwire nawo ntchito inayake. Poopa zimenezi, ndinathawiranso ku Switzerland. Ine ndi banja langa tinakhala kumeneko mpaka mu 1996, pamene tinabwereranso ku Spain.
Panopa mwana wanga wa mwamuna ndiponso mwana wanga wamkazi ali pabanja. Ndipo mwana wanga wa mwamunayo ali ndi ana awiri. Ana angawa ndi mabanja awo akutumikira Yehova. Komanso kwa zaka zonse zimene ndakhala wa Mboni za Yehova ndaphunzitsa anthu okwana 16 kudziwa Yehova. Mmodzi wa anthuwa ndi mnyamata yemwe kale ankachita nawo zinthu zachiwawa ku Spain. Zimenezi zachititsa kuti ndikhale wosangalala kwambiri.
Nthawi zonse ndimapemphera kwa Mulungu kuti andithandize kusiyiratu khalidwe langa lakale komanso kuti ndisamalote zinthu zoopsa. Malangizo a pa Salimo 37:5 andithandiza kwambiri pa moyo wanga. Lembali limati: “Lola kuti Yehova akutsogolere panjira yako, umudalire ndipo iye adzachitapo kanthu.” Ndaona kuti Yehova wachitadi zimenezi kwa ine. Iye wandithandiza kusiya moyo wankhanza. Zimenezi ndi dalitso lalikulu kwambiri kwa ineyo komanso banja langa.
[Chithunzi patsamba 21]
Ndili ndi zaka 13 ku sukulu ya Akatolika yogonera komweko
[Chithunzi patsamba 23]
Ndikutuluka mu ofesi ya asilikali mu 1968, pa nthawi imene ndinasiya ntchito
[Chithunzi patsamba 23]
Ndili ndi mkazi wanga, Encarnita, posachedwapa