N’chifukwa Chiyani Anthu Amachita Zopanda Chilungamo?
PAFUPIFUPI zaka 2,000 zapitazo, Baibulo linaneneratu zimene zidzachitike m’nthawi imene tikukhalayi kuti: “Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, . . . osayamika, osakhulupirika, osakonda achibale awo, osafuna kugwirizana ndi anzawo, . . . osakonda zabwino, achiwembu, osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.”—2 Timoteyo 3:1-4.
Anthu ambiri amavomereza kuti makhalidwe amenewa afala kwambiri masiku ano. Ambiri ndi adyera, atsankho, sakonda anzawo, amakonda ziphuphu ndipo amapondereza anzawo pa nkhani ya zachuma. Tiyeni tione makhalidwe amenewa, lililonse palokha.
DYERA. Anthu ena amanena kuti dyera ndi labwino, koma zimenezi si zoona. Dyera ndi loipa kwambiri. Mwachitsanzo, chifukwa cha dyera anthu amabera makampani ndalama, kuchita mabizinezi achinyengo, ndiponso kubwereketsa ndalama ndi zolinga zadyera. Zimenezi zimachititsa kuti chuma chisamayende bwino ndiponso kuti anthu azivutika. Nthawi zina anthu amene amavutika amakhalanso kuti ndi adyera. Komabe ena amakhala anthu abwinobwino, olimbikira ntchito ndipo ena mwa iwo amalandidwa nyumba ndi ndalama zawo za penshoni.
TSANKHO. Anthu atsankho amachitira ena zopanda chilungamo mwina chifukwa choti akusiyana nawo mtundu, khungu, kuti ndi aamuna kapena aakazi, olemera kapena osauka kapena chifukwa choti ndi osiyana nawo chipembedzo. Mwachitsanzo, komiti ina ya bungwe la United Nations inapeza kuti m’dziko lina ku South America, mayi wina yemwe anali woyembekezera, anamwalira m’chipatala chifukwa chakuti madokotala a chipatala china ankamusala. Mayiyu ankasalidwa chifukwa cha mtundu wake komanso chifukwa chakuti anali wosauka. Tsankho ndi loipa kwambiri chifukwa lingachititse anthu kupha anthu a mtundu wosiyana ndi wawo, mwinanso kufika pofuna kupheratu mtundu wonsewo.
KUSAKONDA ENA. Buku lina linanena kuti: “Chaka chilichonse mabanja ambiri akutha, anthu ambirimbiri akuphedwa komanso katundu wa ndalama zankhaninkhani akuwonongeka chifukwa cha zochita za anthu amene sakonda anzawo. Chiwawa ndiponso zinthu zina zankhanza zili paliponse moti m’tsogolo muno akatswiri ambiri yakale akamadzafotokoza zochitika za m’nthawi yathu ino, sadzanena kuti inali nthawi imene sayansi inapita patsogolo, koma azidzanena kuti inali nthawi imene anthu anasiya kukonda anzawo.” (Handbook of Antisocial Behavior) Buku limeneli linatulutsidwa mu 1997, ndipo mpaka pano zinthu zidakaipiraipirabe.
ZIPHUPHU. Pofotokoza za ziphuphu ku South Africa, magazini ina inanena kuti m’zaka 7 zokha, 81 peresenti ya ndalama zokwana madola 4 biliyoni, zomwe boma linapereka kuti zithandize m’zipatala za m’madera osiyanasiyana zinalowa m’matumba a anthu akatangale. Magaziniyi inanenanso kuti ndalamazo “zinkayenera kugwiritsidwa ntchito yokonzanso zipatala za m’maderawo.”—The Public Manager.
KUPONDEREZANA PA ZACHUMA. Magazini ya Time inanena kuti m’chaka cha 2005, pafupifupi 30 peresenti ya ndalama zonse zimene boma la Britain linapeza “zinalowa m’matumba mwa anthu olemera kwambiri.” Magaziniyi inanenanso kuti ku America, “33 peresenti ya ndalama zimene bomalo linapeza zinalowa m’matumba mwa anthu olemera kwambiri.” Pa tsiku, anthu pafupifupi 1.4 biliyoni padziko lonse amagwiritsa ntchito ndalama zongokwana madola 1.25 kapena kucheperapo ndipo ana 25,000 amamwalira tsiku lililonse chifukwa cha umphawi.
Kodi Pali Njira Yothetsera Kupanda Chilungamo?
M’chaka cha 1987, nduna yaikulu ya dziko la Australia inati ikufuna kuti pofika m’chaka cha 1990, pasadzapezeke mwana aliyense m’dzikolo akuvutika ndi umphawi. Koma chomvetsa chisoni n’chakuti zimenezi sizinatheke. Ndipotu patapita nthawi ndunayi inazindikira kuti inalakwitsa kuikiratu chaka chimene inkayembekezera kuti mavutowa adzatha.
Kunena zoona, kaya munthu ali ndi mphamvu zotani, kaya ndi wolemera bwanji, kaya anthu amamukonda bwanji, munthu ndi munthu basi, sangakwanitse kuthetsa mavuto. Ndipotu ngakhale anthu otchuka kapena olemera amavutika ndi kupanda chilungamo, amakalamba komanso kufa. Zinthu zimenezi zikutikumbutsa malemba awiri a m’Baibulo otsatirawa:
“Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.
“Musamakhulupirire anthu olemekezeka, . . . amene alibe chipulumutso.”—Salimo 146:3.
Ngati timakhulupirira mawu amenewa, sitingadabwe tikamaona anthu akulephera kuthetsa mavuto. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti palibe njira iliyonse yothetsera mavuto? Ayi. Ndipo m’nkhani yomaliza ya nkhani zino, tiona kuti dziko latsopano latsala pang’ono kubwera. M’dziko limeneli mudzakhala chilungamo. Komabe padakali pano zimene ifeyo tingachite ndi kuunikanso zimene timachita komanso zimene timaganiza. Mwachitsanzo, tingadzifunse kuti: ‘Kodi pali zimene ndingachite kuti ndiziyesetsa kuchitira ena zinthu mwachilungamo? Kodi pali zinthu zina zimene ndikufunika kusintha?’ Mafunso amenewa ayankhidwa m’nkhani yotsatira.
[Zithunzi pamasamba 4, 5]
A. Apolisi a ku China atagwira munthu amene ankachita nawo zachiwawa chifukwa chodana ndi anthu amtundu wina
B. Anthu akuwononga komanso kuba katundu mumzinda wa London, ku England
C. Anthu othawa kwawo chifukwa cha nkhondo akuvutika ndi umphawi wadzaoneni pamsasa wina ku Rwanda
[Mawu a Chithunzi]
Top left: © Adam Dean/Panos Pictures; top center: © Matthew Aslett/Demotix/CORBIS; top right: © David Turnley/CORBIS