-
N’chifukwa Chiyani Anthu Amakonda Kugula Katundu Wambirimbiri?Galamukani!—2013 | June
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO: KODI N’KULAKWA KUGULA KATUNDU WAMBIRIMBIRI?
N’chifukwa Chiyani Anthu Amakonda Kugula Katundu Wambirimbiri?
Lipoti limene linatulutsidwa mu 2012, lonena za kafukufuku amene anachitika padziko lonse, linasonyeza kuti hafu ya anthu amene anafunsidwa anavomereza kuti anagulapo zinthu zimene sizinali zofunika kwenikweni. Lipotilo linasonyezanso kuti anthu awiri pa atatu alionse amaona kuti anthu akumakonda kugula katundu wambiri. Zimenezi n’zoona chifukwa anthu ambiri akumakhala ndi ngongole zomwe akulephera kuzibweza. Akatswiri amene anachita kafukufukuyo ananena kuti kugula zinthu zambiri kumapangitsa munthu kukhala ndi nkhawa komanso amakhala wosasangalala. Nanga n’chiyani chimapangitsa kuti anthu azigula katundu wambirimbiri?
ANTHU amalonda amatsatsa makasitomala zinthu zosiyanasiyana. Koma kodi cholinga chawo chimakhala chiyani kwenikweni? Amafuna kuti anthu aziona zinthu zosafunika kwenikweni ngati zofunika kwambiri pamoyo wawo. Otsatsa malonda amadziwanso kuti nthawi zambiri anthu amagula katundu ngati akopeka naye. Ndiye amatsatsa malonda awo kapena amaika katundu wawo m’shopu mokopa makasitomala.
Buku lina linanena kuti: “Anthu ambiri akafuna kugula chinthu, amadziona m’maganizo mwawo akufunafuna chinthucho m’shopu, atachipeza kenako chitakhala chawo.” (Why People Buy Things They Don’t Need) Akatswiri ena amanena kuti anthu ena amasangalala kwambiri akamagula zinthu moti amangogula zinthu mosaganizira. Katswiri wina woona za malonda, dzina lake Jim Pooler, ananena kuti: “Wogulitsa malonda akaona kuti kasitomala wakomedwa amatengerapo mwayi n’kumunyengerera kuti agule katundu wambiri.”
Kodi mungatani kuti ogulitsa malonda asamakunyengerereni kuti mugule katundu amene simunakonzekere kugula? Musamangokomedwa ndi kugula katunduyo ndipo muziganizira ngati zimene amalondawo akunena zili zoona.
AMALONDA AMAFUNA TIZIGANIZA KUTI: Tikagula katundu wambiri tikhala ndi moyo wosangalala
Aliyense amafuna kukhala ndi moyo wosangalala. Amalonda amafuna tiziganiza kuti tikagula katundu wawo ndiye kuti tikhala ndi thanzi labwino, tikhala otetezeka, opanda nkhawa komanso tizikondana kwambiri ndi achibale komanso anzathu.
ZOONA ZAKE:
Nthawi zambiri munthu akakhala ndi katundu wochuluka sasangalala. Tikutero chifukwa chakuti pamafunika nthawi komanso ndalama zambiri zosamalirira katunduyo. Komanso munthuyo amakhala ndi nkhawa chifukwa cha ngongole ndipo sakhala ndi nthawi yokwanira yocheza ndi achibale komanso anzake.
Mfundo yofunika kuiganizira: “Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.”—Luka 12:15.
AMALONDA AMAFUNA TIZIGANIZA KUTI: Tikagula katundu wambiri anzathu azitisirira
Si onse amene amavomera kuti amagula katundu wambiri n’cholinga choti anzawo aziwasirira. Koma Jim Pooler ananena kuti: “Nthawi zambiri anthu akamagula zinthu amakhala ndi cholinga choti anzawo, aneba awo, anzawo akuntchito komanso achibale awo aziwasirira.” N’chifukwa chake amalonda amagwiritsa ntchito anthu otchuka komanso olemera potsatsa malonda awo. Iwo amafuna anthu aziganiza kuti: “Ndikagula katunduyu ndifanana ndi munthu wolemerayo.”
ZOONA ZAKE:
Munthu akamachita zinthu podziyerekezera ndi anthu ena sakhutira ndi zimene alinazo. Amati akapeza zimene amafuna amayambanso kufuna zinthu zina zatsopano.
Mfundo yofunika kuiganizira: “Munthu wokonda siliva sakhutira ndi siliva.”—Mlaliki 5:10.
AMALONDA AMAFUNA TIZIGANIZA KUTI: Tikagula katundu wambiri tikhala otchuka
Buku lina linanena kuti: “Njira yabwino yodziwitsira anthu kuti siiwe munthu wamba (kapena sukufuna kukhala munthu wamba) ndi kugula zinthu zambiri komanso zapamwamba.” (Shiny Objects) Amalonda amadziwa zimenezi choncho iwo amayesetsa kupanga katundu wapamwamba woti anthu akagula azidziona kuti ndi anthu apamwamba.
Kodi inuyo mumadziona kuti ndinu munthu wotani? Nanga mumafuna kuti anthu azikuonani kuti ndinu munthu wotani? Kodi mumafuna kuti anthu azikuonani kuti ndinu munthu wokonda mafashoni? Kapena mumafuna azikuonani kuti ndinu wotchuka ngati osewera mpira? Amalonda amafuna muziganiza kuti mukagula katundu wapamwamba kwambiri anthu azikuonani kuti ndinu munthu wapamwamba.
ZOONA ZAKE:
Ngakhale katundu atakhala wapamwamba bwanji, sangathandize munthu kukhala ndi makhalidwe abwino monga kuona mtima komanso kukhulupirika.
Mfundo yofunika kuiganizira: “Kudzikongoletsa kwanu kusakhale . . . kuvala zodzikongoletsera zagolide, kapena kuvala malaya ovala pamwamba. Koma kukhale kwa munthu wobisika wamumtima.”—1 Petulo 3:3, 4.
-
-
Kodi Mungatani Kuti Musamangogula Zinthu Mwachisawawa?Galamukani!—2013 | June
-
-
Kodi Mungatani Kuti Musamangogula Zinthu Mwachisawawa?
N’zoona kuti nthawi zina timagula zinthu chifukwa chokopedwa ndi otsatsa malonda. Koma kawirikawiri anthufe timagula zinthu chifukwa chotsanzira mtima basi. Tiyeni tikambirane mfundo 6 zimene zingathandize kuti tisamangogula zinthu mwachisawawa.
Musamangogula chifukwa chakuti mwaziona. Kodi mumakonda kugula zinthu makamaka zimene azitsitsa mtengo? Ngati ndi choncho ndiye kuti mwina nthawi zina mumagula zinthu musanaganizire bwino. Kuti mupewe zimenezi, muziganizira kaye mavuto amene angabwere chifukwa chogula zinthuzo. Muziganiziranso mavuto amene nthawi ina munakumana nawo mutagula chinthu mopupuluma. Choncho mukaona chinthu chinachake muzikhala kaye phee, kuganizira ngati mukufunikiradi kuchigula.
Musamagule zinthu kungoti musangalale. Anthu ena amati akakhumudwa, amangopita kukagula zinthu n’cholinga choti asangalaleko ndipo amasangalaladi. Koma amangosangalala kwa nthawi yochepa chifukwa akakhumudwanso amafuna kuti akagule katundu winanso wambiri. Choncho mukakhumudwa muzipeza anzanu amene mungawauze nkhawa zanu kapena muzichita zinthu zina zolimbitsa thupi monga kupita kokayenda.
Musamangogula zinthu chifukwa chakuti mukusowa chochita. Anthu ena amapita kumalo komwe amagulitsa zinthu zapamwamba n’cholinga choti akangoona zinthu basi. Koma dziwani kuti zimene mungakaonezo zingakupangitseni kuti mufune kugula katunduyo. Choncho muzipita kushopu kapena kumsika pokhapokha ngati mukufunadi kugula chinthu chinachake ndipo muzionetsetsa kuti mwangogula chimene mwapitiracho.
Muzisankha mwanzeru anthu ocheza nawo. Zimene anzanu amakonda kuchita komanso kulankhula zimakhudza kwambiri zimene inuyo mumachita. Ngati mumagula katundu wambiri n’cholinga choti mufanane ndi anzanu, mungachite bwino kusiya kucheza nawo n’kupeza anzanu amene sakonda kugula zinthu zambiri.
Musamakonde kugula zinthu pangongole. Munthu akazolowera kugula zinthu pangongole amakhoza kugula zinthu zambirimbiri osaganizira za mtengo wa zinthuzo. Ngati mwatenga zinthu pangongole muziyesetsa kubweza ngongole yonse pakutha pa mwezi. Mukafuna kugula zinthu zofuna ndalama zambiri muziyesetsa kusunga ndalama, n’kudzapereka kamodzi m’malo mogula pangongole.
Muzidziwa mmene ndalama zanu zikuyendera. Ngati simukudziwa mmene ndalama zanu zikuyendera mukhoza kumangogula zinthu zambirimbiri. Choncho muzidziwa kuti mukugwiritsa ntchito ndalama zochuluka bwanji komanso mukutsala ndi zochuluka bwanji. Mungachite bwino kulemba bajeti. Pakutha pa mwezi muziona kuti mwawononga ndalama zingati ndipo muziyerekezera ndi bajeti imene munalemba. Ngati pali zinthu zina zomwe simuzimvetsa bwino, zokhudza kagwiritsidwe ntchito ka ndalama, funsani mnzanu amene mumamudalira kuti akuthandize.
-