Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 9/15 tsamba 7
  • Nkhani za ku Middle East

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nkhani za ku Middle East
  • Galamukani!—2015
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Anthu a ku Kanani Ankapanga Vinyo
  • Kukwera kwa Chiwerengero cha Anthu
  • Anapeza Ndalama Zomwe Zinabisidwa
  • Kodi Mulungu Amatsutsa Kumwa Zakumwa Zoledzeretsa?
    Galamukani!—1991
  • Chozizwitsa Choyamba Chimene Yesu Anachita
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Zakumwa Zoledzeretsa Nchiyani Chomwe Chiri Kawonedwe Kachikristu ka Izo?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Chozizwitsa Choyamba cha Yesu
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
Onani Zambiri
Galamukani!—2015
g 9/15 tsamba 7
Anthu ambirimbiri akuyenda mu msewu wokhala ndi masitolo ambiri ku Middle East

ZOCHITIKA PADZIKOLI

Nkhani za ku Middle East

Ku Middle East n’kumene kale kunali maufumu ambiri. Akatswiri ofukula zinthu zakale apeza zinthu zambiri zakale kudera limeneli.

Anthu a ku Kanani Ankapanga Vinyo

Mitsuko itatu

Mu 2013, akatswiri ofukula zinthu zakale anatulukira chipinda cha pansi pa nthaka ku Kanani. Chipindachi chinali chosungiramo vinyo zaka 3,700 zapitazo. M’chipindamo anapezamo mitsuko ikuluikulu ya vinyo yokwana 40 ndipo vinyo yemwe ankasungidwamo ndi wofanana ndi vinyo yemwe angakwane m’mabotolo 3,000 a masiku ano. Akatswiri omwe anafufuza zotsalira zomwe zinali m’mitsukoyi anapeza kuti anthu a ku Kanani anali akatswiri opanga vinyo. Katswiri wina wofukula zinthu zakale anati: “Zimene anthu a ku Kanani ankathira akamapanga vinyo komanso njira zimene ankatsatira popanga vinyoyu, zinkakhala zofanana.”

KODI MUKUDZIWA? Baibulo limanena kuti anthu akale a ku Isiraeli ankapanga “vinyo wabwino kwambiri” komanso kuti ankamusunga m’mitsuko ikuluikulu.—Nyimbo ya Solomo 7:9; Yeremiya 13:12.

Kukwera kwa Chiwerengero cha Anthu

Nyuzipepala ina inanena kuti chiwerengero cha ana omwe anabadwa ku Egypt mu 2012 chinawonjezeka ndi 560,000 kuposa ana omwe anabadwa mu 2010. (Guardian) Magued Osman yemwe ali m’bungwe lina la kafukufuku ku Egypt anati: “Kuyambira kale, zimenezi sizinachitikepo.” Akatswiri ena akunena kuti ngati chiwerengero cha ana obadwa chitapitiriza kukwera chonchi, dziko la Egypt likhoza kudzakumana ndi mavuto monga kusowa kwa madzi, chakudya komanso magetsi.

KODI MUKUDZIWA? Baibulo limanena kuti Mulungu ankafuna kuti anthu ‘adzaze dziko lapansi,’ koma osati achite kuchulukana n’kufika pomasowa zinthu zofunika pa moyo.—Genesis 1:28; Salimo 72:16.

Anapeza Ndalama Zomwe Zinabisidwa

Ndalama zamkuwa zoposa 100 zomwe zinalembedwa kuti, “Chaka cha 4,” zinapezeka pafupi ndi msewu wina ku Israel. Akatswiri anapeza kuti ndalamazi ziyenera kuti zinabisidwa m’chaka cha 4, Ayuda ataukira ufumu wa Roma, zomwe zinachititsa kuti Yerusalemu awonongedwe. Mkulu wina yemwe ankayang’anira ntchito yokumba pamene panali ndalamazi, dzina lake Pablo Betzer anati: “N’kutheka kuti munthu wina ataona kuti asilikali a Roma akufuna kuwononga mzinda wa Yerusalemu, anabisa ndalamazi poganiza kuti adzabweranso kudzazitenga.”

KODI MUKUDZIWA? M’chaka cha 33 C.E., Yesu ananeneratu kuti asilikali a Roma adzazungulira mzinda wa Yerusalemu. Ananena kuti Akhristu ayenera kuthawira kumapiri kuti adzapulumuke.—Luka 21:20-24.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena