NKHANI YA PACHIKUTO | KODI ZINTHU PADZIKOLI ZAFIKA POIPA KWAMBIRI
Kodi Zinthu Padzikoli Zafika Poipa Kwambiri Kapena Ayi?
PAMENE chaka cha 2017 chinkayamba, gulu la akatswiri a sayansi linapereka uthenga wochititsa mantha. M’mwezi wa January, a sayansiwa analengeza kuti dziko lapansili latsala pang’ono kutha. Akatswiriwa ali ndi wotchi yongoyerekezera yosonyeza nthawi imene yatsala kuti dzikoli lithe ndipo anasunthira kutsogolo muvi wa maminitsi wa wotchiyi ndi masekondi 30. Wotchiyi ataikokera, inayamba kusonyeza kuti kwatsala 2 minitsi ndi hafu kuti nthawi ikwane 12 koloko ya usiku yomwe amati ikuimira nthawi yomwe dzikoli lidzathe. Panopa nthawiyi imaoneka yaifupi kwambiri poyerekeza ndi mmene inkaonekera chikhazikitsireni wotchiyi zaka zoposa 60 zapitazo.
Akatswiri asayansiwa akuganiza kuti mu 2018 adzaonenso kuti nthawi yoti dzikoli lithe yayandikira bwanji. Koma kodi wotchiyo idzawathandizadi kudziwa kuti dzikoli litha liti? Inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinthu padzikoli zafikiratu poipa kwambiri? Mwina mukuona kuti funsoli ndi lovuta kuyankha. Koma si inu nokha, ngakhalenso akatswiri ali ndi maganizo osiyana pa nkhaniyi chifukwa si onse omwe amakhulupirira kuti nthawi ina dzikoli lidzatha.
Pali anthu enanso ambiri omwe amaona kuti zinthu zidzakhala bwino mtsogolo. Anthuwa amanena kuti pali umboni woti anthufe komanso dzikoli lidzakhalapobe mpaka kalekale. Amanenanso kuti pa nthawiyo moyo wa anthu udzakhala wabwino kwambiri. Kodi umboni wa anthuwa ndi womveka? Kodi zinthu padzikoli zafikadi poipa kwambiri?