MUNGATANI KUTI MUCHEPETSE NKHAWA?
N’zotheka Kudzakhala ndi Moyo Wopanda Nkhawa
Mfundo za m’Baibulo zingatithandize kuti tisamakhale ndi nkhawa zosafunikira kwenikweni. Ndi zoona kuti patokha sitingathetseretu zinthu zomwe zimatidetsa nkhawa. Koma Mulungu ali ndi mphamvu yochita zimenezi. Iye anasankha Yesu Khristu kuti adzatichotsere zinthu zonse zomwe zimatipangitsa kukhala ndi nkhawa. Posachedwapa, Yesu adzachita zinthu zambiri zodabwitsa padziko lonse kuposa zimene anachita m’mbuyomu. Mwachitsanzo, iye adzachita zotsatirazi:
ADZACHIRITSA ODWALA NGATI MMENE ANACHITIRA ALI PADZIKOLI.
“Anthu anamubweretsera onse amene anali . . . kuvutika ndi matenda komanso zowawa zamitundumitundu . . . ndipo iye anawachiritsa.”—MATEYU 4:24.
ADZAPEREKA NYUMBA KOMANSO CHAKUDYA KWA ONSE.
“Iwo [olamuliridwa ndi Yesu] adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake. Sadzamanga wina n’kukhalamo. Sadzabzala wina n’kudya.”—YESAYA 65:21, 22.
ULAMULIRO WAKE UDZABWERETSA MTENDERE NDI CHITETEZO PADZIKO LONSE.
“M’masiku ake, wolungama adzaphuka, ndipo padzakhala mtendere wochuluka kwa nthawi yonse pamene mwezi udzakhalepo. Ndipo adzakhala ndi anthu omugonjera kuchokera kunyanja kukafika kunyanja, komanso kuchokera ku mtsinje kukafika kumalekezero a dziko lapansi. . . . Ndipo adani ake adzabwira fumbi.”—SALIMO 72:7-9.
ADZATHETSA ZOPANDA CHILUNGAMO.
“Adzamvera chisoni munthu wonyozeka ndi wosauka, ndipo adzapulumutsa miyoyo ya anthu osauka. Adzawombola miyoyo yawo ku chipsinjo ndi chiwawa.”—SALIMO 72:13, 14.
ADZATHETSANSO MAVUTO NDI IMFA
“Imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—CHIVUMBULUTSO 21:4.