Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • dg gawo 2 tsamba 3-4
  • Dziko Lapansi Lopanda Kuvutika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko Lapansi Lopanda Kuvutika
  • Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
    Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
  • Dziko Latsopano Lopanda Mavuto
    Galamukani!—1990
  • Mavuto Onse a Anthu Adzatha Posachedwapa
    Mavuto Onse a Anthu Adzatha Posachedwapa
  • Kupirira Mavuto Kuli Ndi Ubwino Wake
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
dg gawo 2 tsamba 3-4

Chigawo 2

Dziko Lapansi Lopanda Kuvutika

1, 2. Kodi n’lingaliro losiyana lotani limene ambiri ali nalo?

KOMABE, anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse lapansi ali ndi lingaliro losiyana kotheratu. Iwo akuwoneratu mtsogolo mokondweretsa kaamba ka mtundu wa anthu. Iwo amati posachedwa pompano padziko lapansi padzakhala dziko lopandiratu kuipa ndi kuvutika. Iwo ali ndi chidaliro chakuti zoipa zidzachotsedwa posachedwa ndipo dziko latsopano kotheratu lidzakhazikitsidwa. Iwo amanenanso kuti maziko a dziko latsopano limeneli akuyalidwa tsopano lino.

2 Anthu amenewa amakhulupilira kuti dziko latsopano lidzakhala lopanda nkhondo, nkhalwe, upandu, chisalungamo, ndi umphaŵi. Lidzakhala dziko lopanda matenda, chisoni, misozi, ndipo ngakhale imfa. Panthaŵiyo anthu adzafikitsidwa kuungwiro ndi kukhala ndi moyo wosatha m’chimwemwe m’paradaiso wa padziko lapansi. Eya, ngakhale akufa adzaukitsidwa ndi kupatsidwa mwayi wakukhala ndi moyo kosatha!

3, 4. Kodi n’chifukwa ninji anthu otero ali ndi chidaliro ponena za lingaliro lawo?

3 Kodi lingaliro lamtsogolo limeneli ndilo loto chabe, kungodzinamiza chabe? Ayi, kutalitali. Ndi lozikidwa pa chikhulupiliro chokhala ndi maziko olimba kotero kuti Paradaiso alinkudzayo n’ngwotsimikizirika. (Ahebri 11:1) Kodi n’chifukwa ninji iwo ali otsimikizira kwambiri? Chifukwa chakuti Mlengi wamphamvuyonse wa chilengedwe chonse walilonjeza.

4 Ponena za malonjezo a Mulungu, Baibulo limati: “Sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu, sanasoŵapo mawu amodzi.” “Mulungu sindiye munthu, kuti aname . . . Kodi ananena osachita?” “Yehova wamakamu walumbira, nati, ndithu monga ndaganiza, chotero chidzachitidwa; ndipo monga ndapanga uphungu chotero udzakhala.”—Yoswa 23:14; Numeri 23:19; Yesaya 14:24.

5. Kodi ndi mafunso otani amene afunikira kuyankhidwa?

5 Komabe, ngati chifuno cha Mulungu chinali kukhazikitsa paradaiso wa padziko lapansi wopanda kuvutika, kodi ndi iko komwe n’chifukwa ninji analola zinthu zoipa kuti ziyambe kuchitika? Kodi n’chifukwa ninji wayembekezera zaka zikwi zisanu ndi chimodzi kufikira tsopano kukonza zolakwikazo? Kodi zaka mazana onse ambiriwo akuvutika sizingasonyeze kuti Mulungu sakutisamaliradi, kapena ngakhale kuti iye kulibe?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena