Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gf phunziro 9 tsamba 15
  • Nanga Mabwenzi a Mulungu Ndani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nanga Mabwenzi a Mulungu Ndani?
  • Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Analenga Angelo Ambirimbiri
    Kodi Mizimu ya Akufa Ilipodi?
  • Angelo Ndiwo “Mizimu Yotumikira Anthu”
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Anthu Akafa Amasanduka Angelo?
    Galamukani!—2006
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!
gf phunziro 9 tsamba 15

PHUNZIRO 9

Nanga Mabwenzi a Mulungu Ndani?

Yesu Khristu monga Mfumu ndipo angelo akutsogolera ntchito yolalikira

Yesu Kristu ndi Mwana wa Yehova, komanso ndiye bwenzi lake lenileni lapamtima. Asanadzakhale pano padziko lapansi monga munthu, Yesu anali kumwamba monga cholengedwa champhamvu chauzimu. (Yohane 17:5) Kenako anabwera padziko lapansi kudzaphunzitsa anthu choonadi chonena za Mulungu. (Yohane 18:37) Iye anaperekanso moyo wake kuti apulumutse anthu omvera ku uchimo ndi imfa. (Aroma 6:23) Yesu tsopano ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, boma lakumwamba limene lidzabweretsa Paradaiso padziko lapansili.—Chivumbulutso 19:16.

Angelo Alinso mabwenzi a Mulungu. Angelo sanayambe akhalapo anthu padziko lapansi. Mulungu anawalenga iwo kumwambako asanalenge dziko lapansi. (Yobu 38:4-7) Angelo alipo mamiliyoni ambiri. (Danieli 7:10) Mabwenzi a Mulungu akumwamba ameneŵa amafuna kuti anthu aphunzire choonadi chonena za Yehova.—Chivumbulutso 14:6, 7.

A Mboni za Yehova akulalikira kwa mayi wina

Mulungu alinso ndi mabwenzi padziko lapansi; amawatcha Mboni zake. Mboni m’bwalo la milandu imanena zimene imadziŵa ponena za munthu wina kapena chinthu china. Mboni za Yehova zimauza ena zimene zimadziŵa ponena za Yehova ndi chifuno chake. (Yesaya 43:10) Mofanana ndi angelo, Mbonizo zimafuna kukuthandizani kuphunzira choonadi chonena za Yehova. Zimafuna kuti inunso mukhale bwenzi la Mulungu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena