Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • kp tsamba 9-11
  • Kodi Moyo Wanu Ukuloŵera Kuti?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Moyo Wanu Ukuloŵera Kuti?
  • Dikirani!
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
    Galamukani!—2007
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
    Galamukani!—2007
  • Zoti Banja Likambirane
    Galamukani!—2010
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
    Galamukani!—2007
Onani Zambiri
Dikirani!
kp tsamba 9-11

Kodi Moyo Wanu Ukuloŵera Kuti?

• Anthu ambiri ndi otanganidwa kwambiri ndi zochitika pamoyo watsiku ndi tsiku moti saganizira n’komwe kumene moyo wawo ukuloŵera.

• Baibulo limatiuza za zinthu zochititsa chidwi zimene zikubwera kutsogoloku. Limatichenjezanso za kusintha kwakukulu pa mabungwe a anthu padziko lonse lapansi kumene kukubwera. Kuti zinthu zidzatiyendere bwino ndiponso kuti tidzapeŵe tsoka, tikufunika kuchitapo kanthu mwamsanga.

• Pali anthu ena amene amadziŵa zimene Baibulo limanena ndipo amayesetsa kutsatira zimenezi pamoyo wawo koma amalola kuti nkhaŵa za pamoyo ziwadodometse.

• Kodi mukusangalala ndi kumene moyo wanu ukuloŵera? Mukamakonza zochita zinthu zinazake, kodi mumaganizira mmene zimenezi zingakhudzire zolinga zanu za m’tsogolo?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]

Kodi Chofunika Kwambiri kwa Inu N’chiyani?

Kodi zinthu zotsatirazi mungaziike pamalo ati? Zipatseni manambala malinga n’kufunika kwake.

Zambiri mwa zinthu zimenezi n’zofunikira pamoyo, koma mutati musankhe, n’chiyani chimene chimabwera poyamba, pachiŵiri, mpaka pomaliza?

․․․ Zosangalatsa

․․․ Ntchito yanga

․․․ Thanzi langa

․․․ Kukhala wachimwemwe pa moyo wanga

․․․ Mwamuna kapena mkazi wanga

․․․ Makolo anga

․․․ Ana anga

․․․ Nyumba yabwino, zovala zabwino

․․․ Kuchita bwino kuposa aliyense pa chilichonse chimene ndimachita

․․․ Kulambira Mulungu

[Bokosi pamasamba 10, 11]

Kodi Kumene Moyo Wanu Ukuloŵera Chifukwa cha Zosankha Zanu N’kumene Mukufunadi Kupita?

TAGANIZIRANI MAFUNSO OTSATIRAŴA

ZOSANGALATSA: Kodi zosangalatsa zimene ndimasankha zimanditsitsimula? Kodi zimaphatikizapo zosangalatsa zimene zingaike thanzi langa pangozi kapena kundipundula kumene? Kodi ndi “kusangalala” kumene kumangochitika mwina kwa maola ochepa chabe koma kumene kungandibweretsere mavuto kwa nthaŵi yaitali? Ngakhale zosangalatsa zimene ndimasankha zikhale zabwino, kodi ndikutha nthaŵi yaitali pa zosangalatsazo moti sindikukhala ndi nthaŵi yochitira zinthu zofunika kwambiri?

NTCHITO YANGA: Kodi imandithandiza kuti ndizipeza zofunika pamoyo, kapena kodi ndasanduka kapolo wake? Kodi imafuna zambiri zomwe zikuwonongetsa thanzi langa? Kodi ndingasankhe kugwira ntchito yowonjezera pa ntchito yanga, kapena kuthera nthaŵi limodzi ndi mwamuna kapena mkazi wanga, kapenanso ana anga? Ngati abwana anga amafuna kuti ndizichita ntchito yosemphana ndi chikumbumtima changa kapena imene imandidyera nthaŵi yochitira zinthu zauzimu, kodi ndingalole kuchita ntchito yoteroyo kuti asandichotse ntchito?

THANZI LANGA: Kodi sindilisamala, kapena ndimayesetsa kulisamalira nthaŵi zonse? Kodi ndimangokhalira kulankhula za thanzi langa? Kodi mmene ndimasamalira thanzi langa zimasonyeza kuti ndimadera nkhaŵa anthu a m’banja langa?

KUKHALA WACHIMWEMWE PA MOYO WANGA: Kodi ndizo zimakhala poyamba m’moyo wanga? Kodi ndimaika chimwemwe changa poyamba n’kuika chimwemwe cha mwamuna kapena mkazi wanga ndi banja langa kumbuyo? Kodi zimene ndimachita kuti ndikhale ndi chimwemwe pamoyo wanga n’zogwirizana ndi kulambira Mulungu woona?

MWAMUNA KAPENA MKAZI WANGA: Kodi mwamuna kapena mkazi wanga amakhala mnzanga panthaŵi imene zinthu zikomere ineyo basi? Kodi ndimalemekeza mwamuna kapena mkazi wanga monga munthu payekha wofunika kulemekezedwa? Kodi kukhulupirira Mulungu kumatsogolera mmene ndimaonera mwamuna kapena mkazi wanga?

MAKOLO ANGA: Ngati ndikadali mwana, kodi ndimamvera makolo anga? Kodi ndimayankha mwaulemu akamandilankhula? Kodi ndimachita ntchito imene andiuza kuti ndichite? Kodi ndimabwera panyumba panthaŵi imene andiuza kuti ndibwere? Kodi ndimapeŵa kucheza ndi anthu amene andiuza kuti ndisamacheze nawo ndiponso kodi sindichita zinthu zimene andiuza kuti ndisamachite? Ngati ndine munthu wachikulire, kodi ndimamvetsera mwaulemu makolo anga akamalankhula, ndipo kodi ndimawathandiza nthaŵi iliyonse imene akufunikira thandizo? Kodi mmene ndimachitira nawo zinthu zimadalira ngati zinthu zindikomere ineyo kapena ndimatsatira malangizo a m’Mawu a Mulungu?

ANA ANGA: Kodi ndimaona kuti ndili ndi udindo wophunzitsa ana anga makhalidwe oyenera, kapena ndimayembekezera kuti masukulu ndiwo ayenera kuchita zimenezi? Kodi ndimathera nthaŵi limodzi ndi ana anga, kapena ndimayembekezera kuti zidole, TV, kapena kompyuta n’zimene ziziwasangulutsa? Kodi ndimalanga ana anga nthaŵi iliyonse imene sanamvere malamulo a Mulungu, kapena ndimawalanga makamaka akachita chinachake chimene chandikwiyitsa?

NYUMBA YABWINO, ZOVALA ZABWINO: Kodi n’chiyani chimandichititsa kufuna kuti ndizioneka moteremu ndiponso kuti ndikhale ndi katundu amene ndili naye? Kodi ndimafuna kugometsa anthu oyandikana nawo nyumba, kapena kodi ndimachita zimenezi chifukwa cha ubwino wa anthu a m’banja mwanga, kapena chifukwa chakuti ndine munthu wolambira Mulungu?

KUCHITA BWINO KUPOSA ALIYENSE PA CHILICHONSE CHIMENE NDIMACHITA: Kodi ndimaona kuti kuchita zinthu bwino n’kofunika? Kodi ndimayesetsa kuti mpaka ndichite bwino kuposa aliyense? Kodi sindisangalala munthu wina akachita bwino kuposa ineyo?

KULAMBIRA MULUNGU: Kodi kuyanjidwa ndi Mulungu n’kofunika kwambiri kwa ine kuposa kuyanjidwa ndi mwamuna kapena mkazi wanga, ana anga, makolo anga, kapena abwana anga? Pofuna kukhala ndi moyo wopeza bwino, kodi ndingalolere kukankhira utumiki wa Mulungu kumbuyo?

TAGANIZIRANI MOFATSA MALANGIZO A M’BAIBULO

Kodi Mulungu ali ndi malo otani pamoyo wanu?

Mlaliki 12:13: ‘Opa Mulungu, nusunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.’

DZIFUNSENI KUTI: Kodi moyo wanga umasonyeza kuti mmenemo ndi mmene ndimaonera zinthu? Kodi kumvera Mulungu kumanditsogolera posamalira maudindo anga panyumba, kuntchito, kapena kusukulu? Kapena kodi zinthu zina zimene ndimakonda kayanso zovuta za pamoyo n’zimene zimandichititsa kuti ndikhale ndi nthaŵi yochita zinthu za Mulungu kapena ndisakhale nayo?

Kodi muli ndi ubwenzi wotani ndi Mulungu?

Miyambo 3:5, 6: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.”

Mateyu 4:10: “Ambuye Mulungu wako udzam’gwadira, ndipo iye yekhayekha udzam’lambira.”

DZIFUNSENI KUTI: Kodi mmenemo ndi mmene ndimamvera ndikaganizira za Mulungu? Kodi zimene ndimachita tsiku lililonse, komanso zimene ndimachita pakagwa mavuto zimasonyeza kuti ndili ndi chikhulupiriro ndi kudzipereka koteroko?

Kodi kuŵerenga ndi kuphunzira Baibulo n’zofunika motani kwa inu?

Yohane 17:3: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.”

DZIFUNSENI KUTI: Kodi ndimaŵerenga Mawu a Mulungu ndi kuwaganizira kwambiri moti zimasonyeza kuti ndimakhulupiriradi zimenezo?

Kodi kupezeka pa misonkhano ya mpingo wachikristu n’kofunika motani kwa inu?

Ahebri 10:24, 25: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, . . . ndiko koposa monga momwe muona tsiku lili kuyandikira.”

Salmo 122:1: “Ndinakondwera m’mene ananena nane, tiyeni ku nyumba ya Yehova.”

DZIFUNSENI KUTI: Kodi moyo wanga umasonyeza kuti ndimamvera malangizo opezeka m’Mawu a Mulungu ameneŵa? Mwezi wathawu, kodi sindinapite ku misonkhano yachikristu inayake chifukwa chakuti ndinkachita chinachake pa nthaŵi imene ndinayenera kukhala ku misonkhanoyo?

Kodi mumalalikira nawo mwakhama za Mulungu ndi zolinga zake?

Mateyu 24:14: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni . . . ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”

Mateyu 28:19, 20: “Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse. . . ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.”

Salmo 96:2: “Muimbireni Yehova, lemekezani dzina lake; lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.”

DZIFUNSENI KUTI: Kodi ntchito imeneyi ndi yofunikadi pa moyo wanga monga momwe iyenera kukhalira? Kodi zimene ndimachita mu ntchito imeneyi zimasonyeza kuti ndikukhulupiriradi kuopsa kwa masiku amene tikukhala ano?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena