Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yp2 tsamba 33
  • Chitsanzo Chabwino—Msulami

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chitsanzo Chabwino—Msulami
  • Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Nkhani Yofanana
  • Msulami Ndi Chitsanzo Chabwino Kwambiri kwa Atumiki a Yehova
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Otsalira a Asulami
    Imbirani Yehova Zitamando
  • Chikondi Chowona Chiri Chachipambano!
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Mfundo Zazikulu za Nyimbo ya Solomo
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
yp2 tsamba 33

Chitsanzo Chabwino​—Msulami

Mtsikana wachisulami ankadziwa kuti sayenera kungotengeka maganizo pankhani ya chikondi. Iye anauza anzake kuti: ‘Ndikulumbirirani . . . musautse, musagalamutse chikondi, chisanafune mwini.’ Msulamiyu anadziwa kuti munthu angalephere kuganiza bwino chifukwa chongotengeka maganizo. Mwachitsanzo, anazindikira kuti anthu ena akanatha kumulimbikitsa kukhala pachibwenzi ndi munthu amene sakuyenerana naye. Anazindikiranso kuti mtima wake ungamuchititsenso kusaganiza mwanzeru. Choncho Msulamiyu anapitiriza kukhala ngati “khoma.”—Nyimbo ya Solomo 8:4, 10.

Kodi ndinu wokhwima maganizo moti mumaona nkhani ya chikondi ngati mmene Msulami anali kuionera? Kodi mumayamba mwaganiza kaye musanachite zinthu kapena mumangotsatira zimene mtima wanu wafuna? (Miyambo 2:10, 11) Nthawi zina ena angakulimbikitseni kukhala pachibwenzi inuyo musanafike poti n’kuchita zimenezo. Zochita zanunso zingakulowetseni m’vuto limeneli. Mwachitsanzo, mukaona mnyamata ndi mtsikana akuyenda atagwirana manja, kodi nanunso mumalakalaka mutachita zimenezo? Kodi mungafune munthu amene si wachipembedzo chanu? Pankhani zachikondi, mtsikana wachisulami anali wokhwima maganizo. Inunso mungakhale wotero.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena