CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NYIMBO YA SOLOMO 1-8
Msulami Ndi Chitsanzo Chabwino Kwambiri kwa Atumiki a Yehova
N’chifukwa chiyani tinganene kuti mtsikanayu ndi chitsanzo chabwino?
Anali wanzeru ndipo anadikira mpaka atapeza chikondi chenicheni
Sankalola kuti anthu ena amukakamize kuti ayambe chibwenzi ndi munthu wina aliyense
Anali wodzichepetsa, wosakonda chuma komanso wodzisunga
Sanakopeke ndi zinthu ngati golide kapena mawu okopa achikondi
Dzifunseni kuti:
‘Kodi ndi khalidwe liti la mtsikanayu limene ndiyenera kuyesetsa kumutsanzira?’