Kumanzere: Banja la Beteli la ku Brooklyn linakondwerera Khirisimasi komaliza mu 1926; Kumanja: Anthu amaona kuti a Mboni za Yehova ndi anthu osiyana
GAWO 3
Mfundo Zimene Anthu Amene ali mu Ufumuwu Amatsatira—Kufunafuna Chilungamo cha Mulungu
TAYEREKEZERANI kuti tsiku lina mukubayibitsa neba wanu yemwe wakhala akuona zimene banja lanu limachita ndipo naye akukubayibitsani kenako n’kukukodolani. Pamene mukuyamba kucheza naye, akukufunsani kuti: “Kodi n’chifukwa chiyani anthu inu mumachita zinthu mosiyana ndi anthu ena?” Ndiyeno mukumufunsa kuti, “Mukutanthauza chiyani?” Iye akunena kuti, “Ndikudziwa kuti ndinu a Mboni chifukwa mumasiyana ndi anthu amatchalitchi ena. Simumachita nawo zikondwerero zina, simumalowerera nawo ndale, simumamenya nawo nkhondo, simusuta fodya komanso nonse muli ndi makhalidwe abwino kwambiri. N’chifukwa chiyani anthu inu mumachita zinthu mosiyana ndi anthu ena?”
Inuyo mukudziwa kuti yankho lake n’lakuti: Tikulamuliridwa ndi Ufumu wa Mulungu ndipo Yesu, yemwe ndi Mfumu, akupitirizabe kutiyenga. Akutithandiza kuti tizitsatira chitsanzo chake n’cholinga choti tikhale ndi makhalidwe osiyana kwambiri ndi anthu a m’dziko loipali. M’chigawo chimenechi, tiona mmene Ufumu, womwe Mfumu yake ndi Mesiya, wakhala ukuyengera anthu a Mulungu mwauzimu komanso kuti akhale ndi makhalidwe abwino. Ukuwayenganso monga gulu n’cholinga choti anthu onse alemekeze Yehova.