PHUNZIRO 05
Baibulo Ndi Buku Lochokera kwa Mulungu
Baibulo ndi mphatso yapadera imene Yehova watipatsa, ndipo lili ndi mabuku 66. Mwina mungadzifunse kuti: ‘Kodi chinachitika n’chiyani kuti Baibulo likhalepo? Nanga analilemba ndi ndani?’ Kuti tiyankhe mafunso amenewa, tiyeni tikambirane kaye zimene Mulungu anachita kuti uthenga wake wa m’Baibulo utipeze.
1. Popeza anthu ndi amene analemba Baibulo, n’chifukwa chiyani timanena kuti linachokera kwa Mulungu?
Baibulo linalembedwa ndi anthu 40 kwa zaka pafupifupi 1,600 kuchokera mu 1513 B.C.E., kufika mu 98 C.E. Anthu amene analemba Baibulowa ankagwira ntchito zosiyanasiyana. Ngakhale zili choncho, mabuku ake onse ndi ogwirizana. Kodi zimenezi zinatheka bwanji? Zinatheka chifukwa chakuti Mlembi Wamkulu wa Baibulo ndi Mulungu. (Werengani 1 Atesalonika 2:13.) Anthuwo sanalembe maganizo awo. Koma “analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.”a (2 Petulo 1:21) Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu wake woyera pouzira kapena kuti kuchititsa amuna amenewa kuti alembe maganizo ake.—2 Timoteyo 3:16.
2. Kodi munthu aliyense akhoza kupeza Baibulo?
Anthu a ‘m’dziko lililonse, fuko lililonse, chilankhulo chilichonse ndi mtundu uliwonse’ akhoza kupeza uthenga wabwino wa m’Baibulo. (Werengani Chivumbulutso 14:6.) Mulungu anaonetsetsa kuti Baibulo lizipezeka m’zilankhulo zambiri kuposa buku lina lililonse. Pafupifupi munthu aliyense akhoza kupeza Baibulo ndipo zilibe kanthu kuti amakhala kuti kapena amalankhula chilankhulo chiti.
3. Kodi Yehova wateteza bwanji Baibulo kuti lizipezekabe mpaka pano?
Baibulo linalembedwa pazipangizo zosakhalitsa zopangidwa ndi zikopa komanso udzu wa mtundu winawake. Koma anthu okonda Baibulo ankalikopera pamanja mobwerezabwereza ndiponso mosamala. Ngakhale kuti olamulira ena ankafunitsitsa kuti aliwononge, anthu ena analolera kuika moyo wawo pangozi kuti aliteteze. Yehova sanalole kuti chinthu chilichonse kapena munthu aliyense amulepheretse kutiuza uthenga wake. Baibulo limanena kuti: “Mawu a Mulungu wathu adzakhalapo mpaka kalekale.”—Yesaya 40:8.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti muone zimene Mulungu anachita pouzira anthu kuti alembe Baibulo, mmene analitetezera komanso zimene anachita kuti lizipezeka kwa anthu onse.
4. Baibulo limatiuza lokha kuti mlembi wake wamkulu ndi ndani
Onerani VIDIYO. Kenako werengani 2 Timoteyo 3:16, n’kukambirana mafunso otsatirawa:
Ngati anthu ndi amene analemba Baibulo, n’chifukwa chiyani timati ndi Mawu a Mulungu?
Kodi inuyo mukukhulupirira kuti Mulungu anauzira anthu kuti alembe maganizo ake?
Sekilitale angapemphedwe kuti alembe kalata, koma mawu onse a m’kalatayo amakhala a bwana wake. N’chimodzimodzi ndi Baibulo. Anthu ndi amene analilemba koma uthenga wake ndi wochokera kwa Mulungu
5. Baibulo lakumana ndi mavuto ambiri
Popeza Baibulo ndi lochokera kwa Mulungu, n’zosadabwitsa kuti iyeyo analiteteza. Kuyambira kalekale, olamulira amphamvu akhala akuyesetsa kuti awononge Baibulo. Nawonso atsogoleri achipembedzo akhala akuyesetsa kubisa Baibulo kuti anthu asamaliwerenge. Anthu ambiri anaika moyo wawo pangozi kuti ateteze Baibulo ngakhale kuti ankatsutsidwa ndipo akanatha kuphedwa. Kuti mudziwe mmodzi mwa anthu amenewa, onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
Kodi kudziwa kuti anthu anachita zambiri poteteza Baibulo kwakuthandizani kuti muzifuna kuliwerenga? N’chifukwa chiyani mukutero?
Werengani Salimo 119:97, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani anthu ambiri analolera kuika moyo wawo pangozi pogwira ntchito yomasulira ndiponso kufalitsa Baibulo?
6. Buku la anthu onse
Baibulo ndi buku limene lamasuliridwa komanso kufalitsidwa kwambiri kuposa buku lina lililonse. Werengani Machitidwe 10:34, 35, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
N’chifukwa chiyani Mulungu amafuna kuti Mawu ake amasuliridwe ndi kufalitsidwa m’zilankhulo zambiri?
Kodi ndi zinthu ziti zokhudza Baibulo zimene zimakusangalatsani?
Pafupifupi
munthu aliyense
padzikoli
akhoza kupeza Baibulo m’chilankhulo chimene amamva
Baibulo likupezeka m’zilankhulo zoposa
3,000
lathunthu kapena mbali zake zina
Mabaibulo
pafupifupi 5 biliyoni
afalitsidwa
ndipo nambala imeneyi ikuposa buku lina lililonse
ANTHU ENA AMANENA KUTI: “Baibulo ndi buku lakale lolembedwa ndi anthu.”
Kodi inuyo mukuganiza bwanji?
Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Baibulo ndi Mawu a Mulungu, ndipo iye anaonetsetsa kuti anthu onse azitha kulipeza.
Kubwereza
Kodi tikamanena kuti Mulungu anauzira anthu kuti alembe Baibulo timatanthauza chiyani?
N’chiyani chimakuchititsani chidwi mukaganizira zimene zinachitika kuti Baibulo lisawonongedwe, limasuliridwe ndiponso lifalitsidwe?
Kodi mumamva bwanji mukaganizira zimene Mulungu wakuchitirani kuti muzimva mawu ake?
ONANI ZINANSO
Werengani mbiri ya Baibulo kuyambira pamene linali m’mipukutu yakale mpaka panopa.
Onani mmene Baibulo lapulumukira ngakhale kuti panali zinthu zitatu zikuluzikulu zimene zikanachititsa kuti liwonongedwe.
“Baibulo—Buku Limene Linapulumuka M’zambiri” (Nsanja ya Olonda Na. 4 2016)
Onani zimene anthu ena anachita kuti amasulire Baibulo ngakhale kuti zikanaika moyo wawo pangozi.
Baibulo lakhala likukoperedwa komanso kumasuliridwa maulendo ambirimbiri. Kodi inuyo mungatsimikizire bwanji kuti uthenga wake sunasinthe?
“Kodi Baibulo Linasinthidwa Kapena Kusokonezedwa?” (Nkhani yapawebusaiti)
a Mzimu woyera ndi mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito ndipo mu Phunziro 07 tidzamva zambiri pa nkhaniyi.