Abambo
Kodi bambo ali ndi maudindo otani?
De 6:6, 7; Aef 6:4; 1Ti 5:8; Ahe 12:9, 10
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Ge 22:2; 24:1-4—Abulahamu ankakonda kwambiri mwana wake Isaki moti anachita zonse zomwe angathe pothandiza mwana wakeyu kuti akwatire mkazi yemwe ankatumikira Yehova
Mt 13:55; Mko 6:3—Yesu ankatchedwa kuti “mwana wa kalipentala” komanso kuti “kalipentala”; umenewu ndi umboni woti Yosefe anaphunzitsa mwana wakeyu ntchito yomwe iye ankagwira
N’chifukwa chiyani bambo ayenera kukondedwa komanso kulemekezedwa m’banja?
Onaninso Mt 6:9
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Ho 11:1, 4—Yehova anachita zinthu zosonyeza kuti azibambo amawaona kuti ndi ofunika komanso amawalemekeza. Iye anaphunzitsa ndi kusamalira anthu ake mwachikondi ngati mmene bambo amasamalilira ana ake
Lu 15:11-32—Yesu anasonyeza kuti amalemekeza kwambiri azibambo komanso amawaona kuti ndi ofunika. Iye anafotokoza nkhani yomwe imatiphunzitsa kuti Yehova ndi Tate wachikondi amene amakhululukira ochimwa amene alapa