Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
Okondedwa Abale ndi Alongo:
Mu uthenga wake wopita kumpingo wa ku Simuna, Yesu anati: “Usachite mantha ndi mavuto amene ukumane nawo.” (Chiv. 2:10) Popeza kuti tikukhala “mʼtsiku la Ambuye,” mawu olimbikitsa amenewa akutikhudzanso masiku ano. (Chiv. 1:10) Tikukhaladi mu “nthawi yapadera komanso yovuta.” (2 Tim. 3:1-5) Choncho timalimbikitsidwa kwambiri kuona anthu a Mulungu padziko lonse akuyesetsa kusonyeza chikhulupiriro komanso kulimba mtima kuti akhalebe okhulupirika akamakumana ndi mayesero.
Koma kodi tingatani kuti tikhalebe okhulupirika komanso kuti ‘tisabwerere mʼmbuyo’ chifukwa cha mantha? (Aheb. 10:39) Popeza timatsutsidwa ngakhalenso kuzunzidwa, sizingakhale zophweka kukhalabe okhulupirika. Komabe aliyense ali ndi ufulu wosankha pa nkhaniyi. Kaya ndife amanyazi kapena olimba mtima, tingasankhe kukhala kumbali ya Yehova n’kumachita zoyenera molimba mtima. Kodi n’chiyani chingatithandize kuchita zimenezi?
M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za amuna ndi akazi omwe anasonyeza kulimba mtima ndipo zingakuthandizeni kuti nanunso mukhale olimba mtima. Baibulo linalembedwa kuti litithandize kuganizira zitsanzo za anthu amenewa n’kumazitsatira. Mukamawerenga nkhanizi, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kuona mmene zitsanzozi zingakuthandizireni pa mavuto amene mukukumana nawo panopa komanso amene mungadzakumane nawo m’tsogolo. Muziganizira mmene Yehova angakuthandizireni kukhala olimba mtima. Muziganiziranso mmene kulimba mtima kwa anthu amenewa kungakuthandizireni pa mfundo zotsatirazi:
Kukhala okonzeka kusintha. (Yak. 3:17) Yehova atakana Sauli, anasankha Davide yemwe anali mnyamata kuti akhale mfumu yotsatira. Ndiyeno Yonatani anasonyeza kukhulupirika ndiponso kulimba mtima povomereza zimene Yehova anasankha ndipo anathandiza Davide ndi mtima wake wonse.
Kutsatira mokhulupirika mfundo zolungama za Yehova. (Aheb. 11:32-34) Hananiya, Misayeli ndi Azariya anali okonzeka kuponyedwa mung’anjo yamoto m’malo mogonja n’kulambira mafano.
Kulankhula zoona zokhudza Yehova ndi Yesu. (Mat. 22:16) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Saulo wa ku Tariso. Iye ankalankhula zoona zokhudza Yesu kwa anthu amene ankayembekezera kuti iyeyo aziwathandiza kuzunza Akhristu.
Tikukhulupirira kuti bukuli likuthandizani kuti mukhale ndi chikhulupiriro cholimba komanso olimba mtima kwambiri. (Sal. 27:14) Yehova akudalitseni pamene mukuthandiza anthu am’banja lanu komanso mumpingo wanu kuti nonse mukhale kumbali ya Ufumu wa Mulungu molimba mtima.
Ndife abale anu,
Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova