MAWU OYAMBA
Mukhoza Kukhala Olimba Mtima Kwambiri
1-3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesu anasonyeza kulimba mtima ponena kuti: “Nyamukani, tiyeni tizipita”?
“NYAMUKANI, tiyeni tizipita.” N’kutheka kuti mawu amenewa ndi mawu osonyeza kulimba mtima kwambiri kuposa mawu ena onse omwe ananenedwapo. N’chifukwa chiyani tikutero? Tingapeze yankho lake tikaganizira munthu amene analankhula mawuwa komanso chifukwa chake.—Mat. 26:46.
“Nyamukani, tiyeni tizipita.”—Mat. 26:46
2 Yesu Khristu ndi amene analankhula mawu amenewa ndipo ankauza otsatira ake okhulupirika. Iye anali atanenaponso mawu amenewa m’mbuyomo. (Yoh. 14:31) Koma pa nthawiyi zinthu zinali zitavuta kwambiri. Yesu anali m’munda wa Getsemane kunja kwa mzinda wa Yerusalemu. Unali usiku mwezi ukuwala ndipo Yesu ankadziwa kuti gulu la anthu lonyamula zida likubwera kudzamugwira. Iye anali atatsala pang’ono kukumana ndi mayesero ovuta kwambiri omwe munthu wina aliyense sanakumanepo nawo. Komanso ankadziwa kuti akhala yekha pa nthawi yovutayi.
3 Yesu sanayese kuzemba zinthu zoopsa zimene akanakumana nazo. Ngakhale kuti akanatha kupempha Mulungu kuti amutumizire angelo amphamvu kuti amuteteze, iye sanachite zimenezo. (Mat. 26:53) M’malomwake, anangonena kuti, “Nyamukani, tiyeni tizipita.” Kodi ankatanthauza kuti azipita kuti? Kupita kumene adani ake akamumange, kumuzunza n’kumupha. N’chifukwa chiyani anali wokonzeka kukumana ndi zimenezi? Chifukwa choti ankakonda Atate ake komanso otsatira ake.
4-5. Kodi tingasonyeze bwanji kulimba mtima ngati Yesu, nanga n’chifukwa chiyani kuchita zimenezi n’kofunika?
4 N’zosachita kufunsa kuti Yesu Khristu anali wolimba mtima kwambiri kuposa munthu wina aliyense. Kodi ndinu wotsatira wa Yesu? Ngati ndi choncho, ndiye kuti inunso ndinu wolimba mtima. Akhristu enieni ayenera kukhala olimba mtima. Tikukhala m’dziko lovuta komanso loopsa, choncho tikufunikira kwambiri khalidwe limeneli kuposa kale.
5 Kodi munthu angasonyeze bwanji kulimba mtima ngati Yesu? Anthu ena amaganiza kuti kulimba mtima kumatanthauza kusaopa chilichonse, kuika moyo wawo pangozi mwadala kapenanso kuganiza kuti palibe chimene chingawavulaze. Ena amaganizanso kuti kulimba mtima kumatanthauza kuchita zachiwawa pofuna kusonyeza kuti ndi amphamvu. (Sal. 11:5) Komatu kulimba mtima kumene Yesu anasonyeza si kumeneku. Munthu wolimba mtima ngati Yesu amagwiritsa ntchito mphamvu zake pochita zinthu zimene Mulungu amafuna, kaya zikhale zovuta ngakhalenso zochititsa mantha.
Mungakhale Olimba Mtima Ngati Yesu
6. Ngati tikuona kuti siife olimba mtima, kodi chitsanzo cha Yesu chingatilimbikitse bwanji?
6 Mwina mumakayikira kuti mungakhale olimba mtima ngati Yesu mutakumana ndi mayesero. Ngati ndi choncho, musamaiwale kuti Yesu amachita zinthu moganizira ena. Mofanana ndi Atate ake, Yesu samayembekezera kuti tizichita zoposa zimene tingakwanitse. (Sal. 103:14; Yoh. 14:9) Mwachitsanzo, usiku womwe Yesu anali m’munda wa Getsemane anapempha ophunzira ake kuti asagone, koma iwo anagona. Komabe iye anawauza mokoma mtima kuti: “Zoona, mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.” (Mat. 26:41) Iye ankadziwa komanso kumvetsa zimene sangakwanitse ndipo amadziwanso zimene inuyo simungakwanitse.
7-8. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira otsatira ake?
7 Yesu anasonyezanso kuti ankakhulupirira otsatira ake. Taganizirani mmene iwo anamvera atawauza kuti: “Limbani mtima. Ine ndaligonjetsa dziko.” (Yoh. 16:33) Ponena zimenezi iye anasonyeza kuti sankakayikira kuti ophunzira akewo asonyeza kulimba mtima ngati iyeyo ndipo anachitadi zimenezi. Yesu analankhula mawu akuti “limbani mtima” maulendo angapo. Ananena zimenezi kwa munthu wakufa ziwalo asanamuuze kuti machimo ake akhululukidwa. (Mat. 9:2) Analankhulanso mawuwa atachiritsa mayi wina yemwe anadwala matenda aakulu kwa nthawi yaitali. (Mat. 9:22) Ananenanso zimenezi kwa ophunzira ake powalimbikitsa kuti asaope mphepo yamphamvu. (Mat. 14:27) Ali kumwamba, anauzanso mtumwi Paulo mawu omwewa pamene oweruza okwiya ankafuna kumupha.—Mac. 23:9-11.
8 Masiku ano, Yesu yemwe ndi Mfumu yolimba mtima amatiuzanso mawu omwewa. Iye amafuna kuti tikhale ‘olimba mtima’ ndipo sakayikira kuti tingakwanitse kuchita zimenezi. Atate ake, Yehova amatipatsa zinthu zomwe timafunikira kuti tikwanitse kukhala olimba mtima.
Kodi Baibulo Lingatithandize Bwanji Kukhala Olimba Mtima Kwambiri?
9. Kodi Mawu a Mulungu angatilimbikitse bwanji?
9 Yehova anatisonyeza chikondi poika zitsanzo zambiri m’Mawu ake ouziridwa zomwe zingatithandize kuti tikhale olimba mtima kwambiri. Timapezamo nkhani za amuna, akazi, ana komanso achikulire omwe anakumana ndi zinthu zosiyanasiyana pa moyo wawo. Mofanana ndi Eliya, onsewa anali anthu “ngati ife tomwe.” (Yak. 5:17) Nawonso sanali angwiro, ankalakwitsa zinthu zina komanso ankachita mantha. Ankakumananso ndi mavuto osiyanasiyana ndipo ena ankakumana ndi zinthu zoopsa. Koma mofanana ndi Yesu, iwo sanagonje. Analimba mtima ndipo anatisiyira zitsanzo zomwe zimatilimbikitsa.
10-11. Kodi bukuli likuthandizani kuchita chiyani, nanga mungaligwiritse ntchito bwanji? (Onaninso bokosi lakuti, “Kodi Mungagwiritse Ntchito Bwanji Bukuli Pophunzira Panokha Komanso pa Kulambira kwa Pabanja?”)
10 Bukuli lakonzedwa kuti likuthandizeni kukhala olimba mtima kwambiri. Lili ndi mitu 54 ndipo likuthandizani kuona mmene Yehova anathandizira anthu omwe sanali angwiro ngati inuyo kuti azichita zinthu molimba mtima. Choncho muziwerenga ndime zonse za nkhaniyo, kufufuza mozama komanso kuphunzira zambiri zokhudza munthuyo. Mukamachita zimenezi, mudzawadziwa bwino kwambiri amuna ndi akazi amenewa.
11 Zitsanzo zawo zingatithandize kukhala olimba mtima kwambiri n’cholinga choti tizipirira mavuto omwe tikukumana nawo “masiku otsiriza” ano. (2 Tim. 3:1) Tsiku lililonse tisamaiwale lonjezo la Yehova ili: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pangʼono.” Zimenezi zikugwirizana ndi zimene Paulo ananena. Paja anati: “Tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: ‘Yehova ndi amene amandithandiza. Sindidzaopa.’”—Aheb. 13:5, 6.