8 YOSEFE
Sanagonje Atakumana Ndi Mayesero
ALI wachinyamata, Yosefe ankakondedwa kwambiri ndi bambo ake (a Yakobo) komanso ndi Yehova Mulungu wake. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti sanakumane ndi mavuto aliwonse. Azichimwene ake ankadana naye kwambiri. Chifukwa chakuti bambo ake ankamukonda komanso kumuchitira zinthu zina zapadera, azichimwene ake ankamuchitira nsanje. Yehova atamulotetsa maloto osonyeza kuti nthawi ina banja lawo lidzamugwadira, mkwiyo wa azichimwene ake unakula kwambiri.
Tsiku lina Yosefe ali ndi zaka pafupifupi 17, bambo ake anamutuma kuti akaone ngati azichimwene ake anali bwino ndipo ulendowu unali wamasiku angapo. Atafika, azichimwene ake anamugwira n’kumuponyera m’chitsime chopanda madzi. Iye anawachonderera koma sanamumvere chisoni. Kenako anaganiza zongomugulitsa kwa a malonda omwe ankadutsa ngakhale kuti poyamba anakambirana zoti amuphe. Kenako anakanamiza bambo awo kuti Yosefe wadyedwa ndi chilombo, ngakhale kuti anali atapita chakum’mwera ku Iguputo komwe anakagulitsidwa ngati kapolo kwa Potifara amene anali nduna m’boma la Farao.
Yosefe akanatha kutaya mtima. Koma anakhalabe wolimba mtima ndipo ankagwira ntchito mwakhama. Baibulo limati: “Yehova anali ndi mnyamatayo.” Iye anaonetsetsa kuti pa chilichonse chomwe Yosefe angachite, zinthu zizimuyendera bwino. Potifara anamupatsa udindo woyang’anira nyumba yake ndi zinthu zake zonse.
Panachitikanso nkhani ina yoopsa. “Yosefe anali wooneka bwino ndiponso wa thupi loumbika bwino” moti mkazi wa Potifara anayamba kumusirira. Iye anaonetsa poyera kuti ankamufuna mpaka anamuuza kuti: “Ugone nane.” Makolo ndi achibale a Yosefe anali kutali, ndiye kodi iye akanatani? Komanso anali kapolo wamba choncho mabwana akewo akanatha kumuchita chilichonse. Abwana ake aakazi akanatha kumuzunza kwambiri. Koma kodi Yosefe anakopeka n’kuchita zomwe mkaziyo ankafuna, kapena anakana?
Kodi Yosefe anakwanitsa bwanji kukana kuchita zoipa ngakhale ankadziwa kuti mkazi wa Potifara akanatha kumuzunza?
Baibulo limati: “Ankakana.” Yosefe anauza mkaziyo kuti Potifara ankamukhulupirira kwambiri, choncho sakanamukhumudwitsa. Chochititsanso chidwi ndi choti Yosefe ananena kuti: “Ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi nʼkuchimwira Mulungu?” Chifukwa chakuti Yosefe ankakonda kwambiri Yehova, analimba mtima n’kukana. Koma mkaziyo sanasiye kumuvutitsa. Ankamuuzabe “tsiku ndi tsiku” kuti agone naye. Tsiku lina antchito ena atatalikira, mkaziyo anagwira malaya a Yosefe n’kumuuza kuti: “Ugone nane basi!” Koma Yosefe anangovula malayawo n’kuthawa. Mkaziyo anasungabe malayawo kenako anadzamuonetsa Potifara n’kumuuza kuti Yosefe amafuna kumugwiririra. Potifara anakwiya kwambiri ndipo analamula kuti Yosefe atsekeredwe m’ndende.
Anatsekeredwa m’ndende yamdima ndipo kwakanthawi mapazi ake anamangidwa m’matangadza komanso anamuveka zitsulo m’khosi. (Sal. 105:17, 18) Yosefe akanatayiratu chiyembekezo. Komabe, Yehova sanamusiye ndipo iyenso sanasiye kumudalira. Kundendeko, ankagwira ntchito mwakhama ndipo Yehova anamudalitsa. Pasanapite nthawi, woyang’anira ndende anamupatsa udindo waukulu. Iye anapitirizabe kupirira molimba mtima.
Chifukwa chakuti Yosefe anakhalabe wokhulupirika komanso wolimba mtima, Yehova ankamukonda kwambiri. Patapita nthawi, Mulungu analotetsa Farao maloto awiri onena zam’tsogolo ndipo Yosefe ndi amene anawamasulira. Iye anauza mfumuyo kuti malotowo akutanthauza kuti kudzakhala chakudya chambiri kwa zaka 7, komanso njala kwa zaka zinanso 7. Farao anasangalala n’kupatsa Yosefe udindo woonetsetsa kuti kuli chakudya chokwanira pokonzekera njalayo. Anamupatsanso udindo wokhala wachiwiri kwa iyeyo ndipo Yosefe anakwanitsa kupulumutsa anthu a ku Iguputo komanso banja lake lonse ku njala. Azichimwene ake atabwera kudzagula chakudya, mosadziwa anagwadira Yosefe. Maloto omwe analota ali mwana aja, anakwaniritsidwa. Patapita nthawi, azichimwene ake anasonyeza kuti anasintha n’kukhala anthu abwino. Mchimwene wawo amene ankadana naye poyamba, anawapulumutsa limodzi ndi bambo awo komanso m’badwo wobwera m’tsogolo. Izi zinatheka chifukwa Yosefe anali wolimba mtima komanso anapitirizabe kukhulupirira Yehova.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Yosefe anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. N’chiyani chimatsimikizira kuti zomwe Baibulo limanena zokhudza moyo wa Yosefe ku Iguputo zinachitikadi? (g 11/10 15 ¶2)
2. Kodi Yosefe anadziwa bwanji kuti kuchita chigololo kunali “choipa chachikulu” kwa Yehova? (Gen. 39:9; w22.08 26 ¶2)
3. N’chifukwa chiyani Mulungu analola kuti Yosefe akhale nduna yaikulu ya Iguputo? (w96 5/1 11 ¶4-wcgr) A
Chithunzi A
4. N’chiyani chikusonyeza kuti Yosefe anali adakali ndi chikhulupiriro cholimba ngakhale pomwe anakwanitsa zaka 110? (Gen. 50:25, 26; w07 6/1 28 ¶10-11) B
Chithunzi B
Zomwe Tikuphunzirapo
Tikaona mmene Yosefe anachitira zinthu ndi azichimwene ake, tingaphunzire chiyani ngati Mkhristu mnzathu atatichitira zinthu zopanda chilungamo? (Gen. 45:4, 5; 50:19-21)
Yosefe anali wokhulupirika kwa Yehova ngakhale pamene anali kutali ndi kwawo. Kodi chitsanzo chake chingatithandize bwanji . . .
tikakhala kusukulu? C
Chithunzi C
tikakhala pa ulendo? D
Chithunzi D
tikamagwiritsa ntchito foni kapena zipangizo zina? E
Chithunzi E
Kodi mungatsanzire bwanji kulimba mtima kwa Yosefe?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Yosefe akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Ngakhale kuti Yehova sanateteze Yosefe kuti asakumane ndi mayesero, anamuthandiza kuti akwanitse kuwapirira. Onani mmene angakuthandizireninso inuyo.
“Yehova Amatithandiza Kuti Zinthu Zizitiyendera Bwino” (w23.01 14-19)
Kodi ana angaphunzire chiyani kwa Yosefe anzawo akamawavutitsa?