22 YONATANI
Anafunika Kulimba Mtima Kuti Akhalebe Wokhulupirika
AMUNA awiri ankakwera mofulumira phiri lokhala ndi miyala yambiri komanso zigwembe. Analinso atanyamula zida zankhondo. Ankapita kukalimbana ndi gulu lalikulu la Afilisiti. Yemwe ankatsogolera anali Yonatani, mwana wa Sauli, mfumu yoyamba ya Aisiraeli. Wina anali mnyamata wake yemwe ankamunyamulira zida ndipo anali atalimbikitsidwa ndi mawu a Yonatani akuti: “Palibe chimene chingalepheretse Yehova kupulumutsa pogwiritsa ntchito anthu ambiri kapena ochepa.” Pasanapite nthawi, Yehova anasonyeza kuti mawu a Yonataniwa ndi oona. Ndipo amuna awiriwo anapha asilikali pafupifupi 20. Zimenezi zinathandiza kuti Aisiraeli aphe Afilisiti ambiri.
Nkhaniyi imasonyeza kuti Yonatani anali wolimba mtima. Komatu si nthawi yokhayi pomwe anasonyeza kulimba mtima. Iye anali wokhulupirika ndipo kuti munthu akhale wokhulupirika amafunikanso kulimba mtima. Yonatani anali mwana wokhulupirika wa Sauli. Koma m’kupita kwa nthawi Sauli anayamba kuchita zinthu zoipa ndipo anasiya kumvera Yehova. Yonatani anafunika kulimba mtima kuti akhale wokhulupirika kwa Yehova osati kwa Sauli.
Patapita zaka zambiri, mwina Yonatani ali ndi zaka pafupifupi 50, anakhala mnzake wa Davide yemwe anali wamng’ono kwa iye. Apa n’kuti Davide atangopha kumene Goliyati yemwe anali chimphona cha Afilisiti. N’zosakayikitsa kuti Sauli ndi anthu ena onse anadabwa kwambiri ndipo ankatamanda Davide. Ndiye kodi Yonatani anamva bwanji? Iye sanamuchitire nsanje Davide. M’malomwake anamupatsa zida zake zomenyera nkhondo kuphatikizapo uta. Imeneyi inali mphatso yapadera chifukwa Yonatani anali ndi luso logwiritsa ntchito uta. Ngakhale kuti Yonatani anali wamkulu kuposa Davide ndi zaka 30, analonjezana kuti akhala mabwenzi ndipo panalibe munthu amene akanawalekanitsa.
Yonatani ankafunika kukhala wokhulupirika kwa Mulungu, kuposa mmene akanakhalira wokhulupirika kwa bambo ake
Nayenso Sauli poyamba ankakonda Davide. Koma pasanapite nthawi, chikondi chake chinachepa ndipo anayamba kumuchitira nsanje. Ndipo ankayembekezera kuti Yonatani nayenso azidana ndi Davide. Koma Yonatani anakhalabe wokhulupirika kwa mnzakeyu ngakhale kuti Yehova anasankha Davide kuti adzakhale mfumu m’malo mwa iyeyo. Sauli atanena kuti akufuna kupha Davide, Yonatani anakhalabe kumbali ya mnzakeyu. Pamenepatu anasonyeza kulimba mtima. Ngakhale kuti pa nthawiyi Sauli anali wachikulire, anali adakali msilikali wamphamvu. Nthawi ina Yonatani akulankhula zabwino zokhudza Davide, Sauli ankafuna kupha mwana wakeyu ndi mkondo. Ngakhale kuti mkondowo sunamubaye, Yonatani anakhumudwa kwambiri ndi zimenezi. Iye anapita kwa Davide n’kukamuuza kuti Sauli akufuna kupha Davideyo. Ndipo Yonatani anapempha Davide kuti ngati chinachake chitamuchitikira adzasamalire anthu am’banja lake.
Sauli anachititsa kuti Davide azikhala moyo wothawathawa. Mfumu Sauli ankagwiritsa ntchito asilikali ake kusaka Davide ndipo zimenezi zinachititsa kuti Davideyo azibisala m’malo osiyanasiyana. Ndiye kodi Yonatani ankathandiza nawo kuchita zimenezi? Baibulo silinena kuti ankathandiza nawo, choncho tikukhulupirira kuti sanachite nawo zimenezi. Pa nthawi ina, Yonatani anadziwa kumene Davide ankabisala ndipo anapita kukamuona. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Ankafuna ‘kumuthandiza kuti apeze mphamvu kuchokera kwa Yehova.’ Anauza Davide kuti: “Usachite mantha, chifukwa Sauli bambo anga sakupeza, moti iwe ukhaladi mfumu ya Isiraeli, ndipo ine ndidzakhala wachiwiri kwa iwe.” Kenako anasiyana koma kameneka kanali komaliza kuonana.
Pasanapite nthawi, Yonatani anapita ndi bambo ake kukamenyana ndi Afilisiti omwe anali adani a Aisiraeli. Koma pa nthawiyi n’kuti Sauli atayamba mpatuko ndipo ankakhulupirira zamizimu. Yehova anasiya kudalitsa Sauli. Kunkhondoko Sauli anavulala kwambiri ndipo kenako anadzipha. Komanso ana ake atatu, kuphatikizapo Yonatani, anaphedwa pankhondoyo.
Davide anamva chisoni kwambiri. Anaimba nyimbo yolira komanso yosonyeza mmene ankamukondera mnzake wapamtimayu. Iye anatchula nyimboyo kuti “Uta,” mwina pokumbukira mphatso imene Yonatani anamupatsa zaka zingapo m’mbuyomo. Davide analemba kuti: “Mtima wanga ukuwawa chifukwa cha iwe mchimwene wanga Yonatani. Ndinkakukonda kwambiri.” Iye anasunga lonjezo limene anapangana ndi mnzakeyo. Atakhala mfumu, anafufuza ngati panali aliyense wam’banja la Yonatani ndipo anapeza Mefiboseti yemwe anali wolumala. Davide anatenga Mefiboseti kuti azikhala pafupi ndi Yerusalemu ndipo anamusamalira kwa moyo wake wonse.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Yonatani anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Kodi Afilisiti anali ndani? (w95 2/1 31-wcgr)
2. Kodi mawu akuti “pimu” akusonyeza bwanji kuti nkhani ya m’Baibuloyi ndi yolondola? (w05 3/15 29) A
Chithunzi A: Kamwala ka pimu
3. N’chifukwa chiyani zinali zovuta kudutsa pamalo owolokera a ku Mikimasi? Nanga n’chiyani chinathandiza Yonatani kuti adutse pamalowa? (it “Mikimasi” ¶4-wcgr) B
Todd Bolen/BiblePlaces.com
Chithunzi B: N’kutheka kuti malo awa, ndi pamene panali malo owolokera a ku Mikimasi
Chithunzi B: N’kutheka kuti malo awa, ndi pamene panali malo owolokera a ku Mikimasi
Todd Bolen/BiblePlaces.com
4. Kodi Davide anachita chiyani pokwaniritsa lonjezo lake loti adzasamalira anthu am’banja la Yonatani? (it “Mefiboseti” Na. 2 ¶1-wcgr)
Zomwe Tikuphunzirapo
Yonatani anakhala wokhulupirika kwa Yehova osati kwa Sauli. Kodi nafenso tingakumane ndi zinthu ziti zomwe tingafunike kusonyeza kuti ndife okhulupirika kwa Yehova osati kwa wina aliyense? C
Chithunzi C
Kodi nkhani ya Yonatani ndi Davide ikukuphunzitsani chiyani zokhudza . . .
anzathu?
kudzichepetsa?
kukhulupirika?
Kodi mungatsanzire Yonatani pa nkhani ya kulimba mtima m’njira zinanso ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Yonatani akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
N’chiyani chinathandiza kuti Yonatani ndi Davide azigwirizana kwambiri, nanga ifeyo tingatani kuti tikhale ndi anzathu otero?
Thandizani ana anu kuti adziwe zimene akuphunzirapo pa zimene zinachitika pa moyo wa Yonatani.