25 DAVIDE
Analimba Mtima Kuchita Zoyenera
PA NTHAWI ina, Sauli ankakonda kwambiri Davide komanso kumukhulupirira. Davide ankamunyamulira Sauli zida zake ndiponso anali mkulu wa gulu lake lankhondo. Koma kenako Davide ankakhala moyo wothawathawa chifukwa choti Sauli ankafuna kumupha. Mulungu analonjeza Davide kuti adzakhala mfumu koma pa nthawiyi ankabisala m’chipululu pofuna kupulumutsa moyo wake komanso wa amuna 600 omwe anali naye.
Sauli anasintha kwambiri n’kukhala mfumu yoipa. Iye ankamuchitira kwambiri nsanje Davide ndipo anakwiya moti maulendo angapo ankafuna kumupha. Pa nthawi ina, Davide anali ndi mwayi wopha Mfumu Sauli koma sanachite zimenezo. M’malo moyamikira zimenezi, Sauli sanasiye kufunafuna Davide kuti amuphe. Amuna amumzinda wa Zifi anamupereka Davide poulula kwa Sauli maulendo awiri za malo omwe ankabisala. Zitatero, Sauli ndi gulu lake lankhondo anayamba kusakasaka Davide.
Ndiye kodi Davide anatani? Choyamba, anatumiza amuna ena kukafufuza komwe kunali Sauli. Ngakhale kuti Sauli anali ndi asilikali okwana 3,000 Davide sanatekeseke. Imeneyi ndi nthawi imene analemba mawu akuti: “Taonani! Mulungu ndi amene amandithandiza. Yehova amadalitsa anthu amene akundithandiza.” (Sal. 54:4; kamutu) Choncho Davide anaganiza zopita kumsasa wa Sauli usiku ndipo anapempha munthu wina kuti amuperekeze.
Abisai anadzipereka. Iye anali mwana wa mchemwali wake wa Davide. Anali msilikali wopanda mantha koma nthawi zina ankachita zinthu mopanda chifundo. Davide atafika kumsasa wa Sauli, anapeza aliyense akugona, Yehova ndi amene anachititsa zimenezi. Mfumu Sauli anali komweko, nayenso anali mtulo tofa nato. Palibe amene ankamulondera ndipo mkondo wake unali utazikidwa pafupi ndi mutu wake.
Ndiye kodi Davide akanatani? Zikanakhala zosavuta kuti aphe Sauli. Mwina akanaganiza kuti akachita zimenezi mavuto ake athera pomwepo ndipo akhala mfumu. Abisai ankangodabwa kuti n’chifukwa chiyani Davide akuchedwachedwa. Choncho ananong’oneza Davideyo kuti: “Lero Mulungu wapereka mdani wanu m’manja mwanu. Bwanji ndimubaye ndi mkondo n’kumukhomerera pansi? Ndimubaya kamodzi kokha, sindichita kubwereza kawiri.”
Davide anakumbukira kuti zoterezi zinachitikaponso. M’chipululu cha Eni-gedi, Sauli analowa kuphanga lomwe Davide anabisala. Popeza Sauli sanamuone Davide, zinali zosavuta kuti amuphe. Koma Davide sanachite zimenezi. M’malomwake anangodula kapisi ka chovala cha Sauli. Koma kenako chikumbumtima chake chinayamba kumuvutitsa. Anaona kuti sanachite bwino chifukwa sanalemekeze wodzozedwa wa Yehova.
Usiku umenewo, sizinali zophweka kuti Davide aletse Abisai kuti asaphe Sauli. Nayenso Abisai ankakhala moyo wothawathawa ngati Davide. Komanso n’zosakayikitsa kuti anthu onse amene ankayenda ndi Davide ankafuna nkhanza za Sauli zitatha. Koma Davide anakana kubwezera. Anadzudzula Abisai kuti asaphe Sauli koma akhalebe woleza mtima. Davide anatsimikizira Abisai kuti: “Yehova, Mulungu wamoyo, Yehova adzamulanga yekha [Sauli], kapena tsiku lidzafika ndipo adzamwalira, kapenanso adzapita kunkhondo nʼkukaphedwa.” Anawonjezeranso kuti: “Ndikaiganizira nkhaniyi mmene Yehova akuionera, sindingayerekeze kuvulaza wodzozedwa wa Yehova.”
Kodi Davide anatani atakakamizidwa kuti aphe mdani wake wamphamvu?
Davide ankadziwa kuti Yehova adzalanga Sauli pa nthawi yoyenera. Musalimo lomwe talitchula kale lija, iye analemba zokhudza Yehova kuti: “Iye adzabwezera adani anga zoipa zimene akuchitira anthu ena.” (Sal. 54:5) Choncho Davide ndi Abisai anachoka kumsasa wa Sauli n’kupita chapafupi pamalo ena okwera. Davide anakuwira Sauli ndi asilikali ake. Anakalipira asilikali a Sauli chifukwa cholephera kuteteza mfumu yawo ndipo anadzudzula Sauli chifukwa chotaya nthawi ndi kumusakasaka. Ananena kuti ali ngati “nthata imodzi” imene singachite chilichonse kwa mfumu. Sauli anachita manyazi kwambiri ndipo anavomereza kuti: “Ndachita zinthu mopusa komanso ndalakwitsa kwambiri.”
Ndiye kodi Sauli anasintha? Ayi ndithu. Davide ankadziwa kuti Sauli sanasinthe. Koma sananong’oneze bondo chifukwa chochita zinthu molimba mtima potsatira chikumbumtima chake. Patapita nthawi, Yehova anadalitsa mtumiki wake wolimba mtima komanso wokhulupirikayu m’njira zimene sankaziganizira n’komwe.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana
Malinga ndi nkhaniyi, kodi Davide anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Ngakhale kuti Abisai nthawi zina ankachita zinthu mwaphuma komanso mopanda chifundo, kodi anasonyeza bwanji kulimba mtima poteteza anthu a Yehova komanso Davide? (it “Abisai” ¶3-5-wcgr)
2. N’chifukwa chiyani Davide anadziyerekezera ndi “nkhwali imodzi m’mapiri”? (1 Sam. 26:20; it “Nkhwali” ¶4-wcgr) A
Ekaterina Kolomeets/stock.adobe.com
Chithunzi A
3. N’chifukwa chiyani Davide ankafunika kuleza mtima? (w17.08 6 ¶14-15)
4. N’chifukwa chiyani Davide anafunika kupitiriza kukhala wodzichepetsa ngakhale patadutsa zaka zambiri nkhaniyi itachitika? (w21.09 10 ¶8) B
Chithunzi B
Zomwe Tikuphunzirapo
Ngakhale kuti Sauli ankalakwitsa zinthu zambiri, Davide ankamulemekezabe monga munthu waudindo. Kodi ifeyo tingatsanzire bwanji Davide pa nkhani ya mmene timaonera . . .
makolo athu? C
Chithunzi C
akuluakulu a boma? D
Chithunzi D
akulu mumpingo? E
Chithunzi E
Davide anatsatira molimba mtima chikumbumtima chake. Kodi ndi pa zinthu ziti zimene nafenso tiyenera kutsatira molimba mtima chikumbumtima chathu?
Kodi mungatsanzire Davide pa nkhani ya kulimba mtima m’njira zinanso ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Davide akadzaukitsidwa zokhudza nkhani imeneyi?
Phunzirani Zambiri
Yerekezerani kuti mukuona zimene zafotokozedwa munkhaniyi zikuchitika.
Muzikumbukira Zimene Chikondi Chimachita Komanso Zimene Sichichita—Chimakwirira Zinthu Zonse (1:29)
Kodi ana angaphunzire chiyani kwa Sauli yemwe poyamba anali wodzichepetsa koma kenako anayamba kudzikuza?