31 KAMTSIKANA KA KU ISIRAELI
Kamtsikana Kanalankhula Molimba Mtima Kudziko la Eni
PANALI kamtsikana kena ka ku Isiraeli komwe kanakhalapo ndi moyo pa nthawi ya Mfumu Yehoramu. Dzina lake silidziwika, koma tikudziwa zinthu zothandiza kwambiri zimene kanachita. Mfumuyi komanso anthu amene inkawalamulira anasiya kulambira Yehova mokhulupirika choncho Yehovayo analola kuti Asiriya azibwera kudzamenyana nawo. Tsiku lina Asiriya atabwera, anagwira kamtsikanako n’kupita nako kudziko lawo.
Kamtsikanaka kayenera kuti kanali ndi mantha. Nawonso anthu am’banja lake ayenera kuti anali ndi nkhawa. Kamtsikanaka kanakhala wantchito wa Namani ndi mkazi wake. Namani anali mkulu wa asilikali a Siriya. Mwanayu ayenera kuti anayesetsa kuti azolowere moyo watsopanowu. Koma pasanapite nthawi, anazindikira kuti anthu am’banjali sankasangalala chifukwa panali vuto. Namani anali ndi matenda oopsa akhate. Matendawa ankachititsa munthu kukhala ndi mabala oopsa ndipo nthawi zina sankachira.
Ngakhale kuti anali kapolo m’dziko la anthu osalambira Mulungu, anapitirizabe kusonyeza chifundo komanso kulimba mtima
Kamtsikanaka kanali kokoma mtima kwambiri. Ngakhale kuti kankadziwa zoti Namani anali mdani wa Aisiraeli, kanamvera chisoni Namaniyo ndiponso mkazi wake. Ndipo kankadziwa zoti akhoza kuchira. N’kutheka kuti makolo ake anamufotokozera kuti Yehova anathandiza mneneri wake Elisa kuti achite zinthu zodabwitsa. Koma kamtsikanaka sikankadziwa ngati Elisa anachiritsapo munthu wodwala khate m’mbuyomo. Komabe kankakhulupirira kuti Mulungu wake, Yehova, akhoza kupereka mphamvu kwa mneneri wake zochiritsira Namani.
Koma kodi kakanalimba mtima kuuza banjali zokhudza Yehova ngakhale kankadziwa kuti kuchita zimenezi kunali koopsa? Namani ankalambira mulungu wotchedwa Rimoni ndipo nthawi zonse ankatenga mfumu ya Siriya kupita kukachisi kukalambira mulunguyu. Zikuoneka kuti anthu a ku Siriya ankaona kuti mulunguyu ndi amene ankabweretsa mphepo yamkuntho komanso mabingu. Kodi Namani akanaganiza chiyani zokhudza Yehova, Mulungu wa kamtsikanaka? Kodi mwina akanaona kuti wanyozeka ndi mfundo yoti Yehova akhoza kukwanitsa kuchita zimene mulungu wake walephera kuchita? Kamtsikanaka kayenera kuti kanapemphera kwa Yehova kuti akathandize kulimba mtima. Kenako kanauza abwana ake aakazi kuti: “Abwanawa akanapita kwa mneneri amene ali ku Samariya, bwenzi atakawachiritsa khate lawo.”
Amenewa ndi mawu okhawa amene amapezeka m’Baibulo amene kamtsikanaka kanalankhula. Mawuwa angaoneke ochepa, koma anathandiza kwambiri. Vesi lotsatira limanena kuti Namani anapita kwa mfumu dzina lake Beni-hadadi kukaifotokozera zomwe kamtsikana kaja kananena. Kenako mfumuyo inatumiza Namani ku Isiraeli ndipo inam’patsira kalata kuti akapereke kwa Mfumu Yehoramu yopempha kuti Namaniyo achiritsidwe khate lake.
Namani atachoka, anthu am’banja lake ankayembekezera mwachidwi kuti aone zomwe zingamuchitikire. Kamtsikanako kayenera kuti kankapempha Yehova mobwerezabwereza kuti achitepo kanthu n’cholinga choti Namani adziwe zoti Yehova yekha ndi Mulungu woona. Panadutsa masiku angapo kapenanso mawiki, Namani asanabwere. Koma tsiku lina anatulukira. Tangoganizani mmene anthu am’banjali anasangalalira atamuona. Iye anali atachira. Thupi lake, lomwe linali ndi mabala lija, linali bwinobwino ndipo linali ngati la mnyamata.
Kamtsikanako kayenera kuti kankamvetsera mwachidwi pamene Namani ankafotokoza za ulendo wake. Iye anafotokoza mmene Elisa anamulandirira, mmene anayesedwera pa nkhani ya kudzichepetsa komanso kuti anakwiya. Anafotokozanso kuti atumiki ake ndi amene anamulimbikitsa kuti atsatire malangizo osavuta omwe mneneri Elisa anamuuza. Kenako anafotokoza kuti atakasamba maulendo 7 mumtsinje wa Yorodano, anachira. Koma zomwe zinasangalatsa kwambiri kamtsikanaka n’zakuti Namani atachira, nthawi yomweyo anayamba kulambira Yehova Mulungu.
Zonsezi zinatheka chifukwa kamtsikanaka kanalimba mtima n’kulankhula zokhudza Mulungu komanso mneneri wake. N’zoona kuti sitikudziwa dzina la kamtsikanayu, koma Yehova akulidziwa. Koma ngati tingatsanzire kulimba mtima kwake, Yehova akadzamuukitsa tidzamuona. Tangoganizirani mmene mudzasangalalire kukumana naye, kudziwa dzina lake komanso kumumva akufotokoza zinthu zina zokhudza nkhaniyi.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo
Funso lokambirana:
Kodi kamtsikana ka ku Isiraeli kanasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. N’chifukwa chiyani mwina kamtsikanaka kankachita mantha ndi Asiriya komanso kudabwa ndi zomwe ankachita? (w96 5/15 8 ¶3-wcgr) A
Courtesy of Musée du Louvre, Paris
Chithunzi A: Chidole cha ku Siriya wakale, chomwe mwina chinali mulungu wotchedwa Rimoni
2. Fotokozani zomwe zimachitikira munthu wakhate. (it “Khate” ¶3-5-wcgr)
3. N’chifukwa chiyani Elisa sanalandire mphatso ya Namani? (w05 8/1 9 ¶2)
4. N’chifukwa chiyani Elisa ankakhulupirira kuti Yehova adzakhululukira Namani chifukwa chogwadira mulungu wotchedwa Rimoni? (2 Maf. 5:18, 19; w05 8/1 9 ¶3) B
Chithunzi B
Zomwe Tikuphunzirapo
Namani anali mkulu wa asilikali a Asiriya ndipo anapita kukamenyana ndi Aisiraeli. Komabe Yehova anamuchiritsa. Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani pa mfundo yoti Yehova ndi wachifundo komanso wopanda tsankho? C
Chithunzi C
Kodi chitsanzo cha kamtsikana ka ku Isiraeli chakulimbikitsani bwanji kuti muzilalikira ngakhale pamene mukuchita mantha?
Kodi mungatsanzire kulimba mtima kwa kamtsikana ka ku Isiraeli m’njira zinanso ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzakafunsa chiyani kamtsikana ka ku Isiraeli kakadzaukitsidwa?a
Phunzirani Zambiri
Popeza kamtsikana ka ku Isiraeli sikanatchulidwe dzina, kodi zimenezi zikusonyeza kuti Yehova ankakaona kuti ndi kosafunika?
“N’chifukwa Chiyani Anthu Ena Otchulidwa M’Baibulo Sanatchulidwe Mayina Awo?” (w13 8/1 10)
Onani mmene ana masiku ano angasonyezere kulimba mtima ngati kamtsikana ka ku Isiraeli.
a Ngati mtsikanayu anakula n’kukhala munthu wamkulu, ndiye kuti adzaukitsidwa ali mzimayi.