30 MAYI WAMASIYE WA KU ZAREFATI
Anasonyeza Kulimba Mtima pa Nthawi Yovuta Kwambiri
ANKADZIONA kuti ndi wosafunika ngakhale kuti si mmene zinalili. Kodi pali aliyense amene ankadziwa mavuto ake kapena kumudera nkhawa? Anali mayi wamasiye komanso mayi. Ku Isiraeli, akazi amasiye ankapindula ndi malamulo okoma mtima a Mulungu amene ankateteza akazi ndiponso ana amasiye. Koma mayiyu sanali wa Chiisiraeli. Iye ankakhala ku Zarefati, tauni ya ku Sidoni. Etibaala, yemwe anali mfumu ya ku Sidoni, ayenera kuti anali wansembe wa mulungu wamkazi Asitoreti. Anthu amene ankalambira mulungu ameneyu ankachita makhalidwe oipa osiyanasiyana. M’dziko limeneli, lomwe anthu ankachita zoipa komanso kuvutika ndi chilala ndiponso njala, kodi panali aliyense amene akanasonyeza chifundo mayi wamasiyeyu?
Ankayesetsa kupeza chakudya cha iyeyo ndi mwana wake wamwamuna. Koma zinthu zinkangoipiraipira moti anangotsala ndi kachakudya kochepa kwambiri ndipo zinkaoneka kuti sakhalanso ndi moyo.
Koma panali chinthu chapadera chokhudza mayiyu. Patadutsa zaka pafupifupi 1,000 Yesu Khristu ananena kuti Yehova ankaona kuti mayi ameneyu anali wosiyana ndi anthu opanda chikhulupiriro a ku Isiraeli. Zikuoneka kuti mayiyu anali atamvapo zokhudza Yehova, Mulungu wa Aisiraeli. Mwina anakhudzidwa ndi mmene ankachitira zinthu ndi anthu ake ndipo anayamba kumukhulupirira. Ndiye kodi Yehova akanachita chiyani kwa mayiyu yemwe ankakhala m’dziko lomwe anthu sankalambira Mulungu? Anamuchitira chinthu chapadera kwambiri.
Yehova anauza mneneri wake Eliya kuti apite ku Zarefati n’kumakakhala ndi mayiyu pa nthawi yachilala. Mneneriyu atafika, anapeza mayi wina akutola nkhuni kuti akakoleze moto. Analankhula naye mokoma mtima n’kumupempha kuti: “Mundipatseko madzi pangʼono mʼkapu kuti ndimwe.” Ngakhale kuti mayiyu anali asanamuonepo Eliya, Baibulo limati: ‘Ananyamuka kuti akatenge madziwo.’ N’kutheka kuti mayiyu anazindikira kuti ndi mneneri wa Yehova chifukwa cha mmene analankhulira, mawu ake okoma mtima kapena chovala chake chauneneri. Kodi mayi ameneyu ndi amene Yehova anatuma Eliya kuti adzakumane naye? Kuti adziwe ngati analidi yemweyu, Eliya anamupemphanso mkate.
Atamva zimenezi, mayiyo anati: “Ndikulumbira m’dzina la Yehova Mulungu wanu wamoyo.” Apa anasonyeza kuti ankakhulupirira Mulungu woona, “Mulungu wamoyo.” (Yer. 10:10) Kenako anauza Eliya kuti analibe mkate koma ufa pang’ono mumtsuko waukulu ndi mafuta pang’ono mumtsuko waung’ono. Ankafuna akoleze moto kuti aphike chakudya chomaliza cha iyeyo ndi mwana wake. Iye ananena kuti: “Tikadya, tiziyembekezera kufa.”
Iye ndi mwana wake wamwamuna anali ndi chakudya chodya kamodzi kokha, komabe mneneri wa Yehova anamuuza kuti amukonzere kaye iyeyo chakudya
Koma ayenera kuti anadabwa kwambiri ndi zimene Eliya ananena. Iye anati: “Musaope.” Kodi zikanatheka bwanji kuti asaope popeza ankayembekezera kuona mwana wake akufa ndi njala? Komabe anamvera. Kenako Eliya anamuuza zimene Yehova analonjeza. Analonjeza kuti ngati angayambe kaye wakonzera chakudya mneneriyu, Yehova amudalitsa. Achititsa kuti mtsuko wake wa ufa mukhalebe ufa komanso wa mafuta mukhalebe mafuta pa nthawi yonse yachilala.
Apatu chikhulupiriro cha mayi wamasiyeyu chinayesedwa. Kodi akanatengadi chakudya chochepa chomwe chinatsala n’kupatsa mneneri wa Yehova? Iye ankadziwa kuti Yehova anali atachitirapo anthu ake zinthu zambiri zodabwitsa kuposa kudyetsa mkazi mmodzi wamasiye ndi mwana wake. Koma kodi akanalimbadi mtima n’kuchita zimene mneneriyu anamuuza? Baibulo limati: “Mayiyo anapita nʼkukachita zimene Eliya ananena.”
Yehova anamudalitsa kwambiri. Modabwitsa, ufa ndi mafuta a mayiyo sizinathe moti iyeyo, mwana wake ndi Eliya anapitirizabe kugwiritsa ntchito zinthuzo mpaka chilala chinatha. Yehova anamuchitiranso chinthu china chodabwitsa. Mwadzidzidzi mwana wake anadwala kenako n’kumwalira. Koma Yehova anagwiritsa ntchito Eliya kuukitsa mwanayo. Imeneyi ndi nkhani yoyamba kulembedwa m’Baibulo yonena za munthu amene anaukitsidwa. N’zosakayikitsa kuti zimenezi zinapangitsa kuti chikhulupiriro cha mayiyu chilimbe kwambiri. Mpaka pano chitsanzo cha mayiyu chimathandiza anthu ambiri kukhala olimba mtima.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi mayi wamasiye wa ku Zarefati anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Fotokozani zokhudza chipembedzo cha anthu a ku Sidoni, mzinda waukulu wa ku Foinike. Kodi chipembedzo chimenechi chinakhudza bwanji Aisiraeli? (it “Sidoni” ¶6-wcgr) A
Penta Springs Limited/Alamy Stock Photo
Chithunzi A: Chithunzi cha mulungu wotchedwa Asitoreti cha m’ma 1500 B.C.E.
2. Kodi panali ubale wotani pakati pa Etibaala ndi Mfumu Ahabu ya ku Isiraeli? (it “Etibaala”-wcgr)
3. Anthu a ku Foinike ankalambira mulungu wamkazi wotchedwa Asitoreti (Asitate). Kodi ndi miyambo iti imene ankachita pa kulambira kwawo yomwe imachitikanso masiku ano? (g93 12/8 21 ¶1-4-wcgr)
4. Pamene mwana wamwamuna wa mayi wamasiye anamwalira, mwina n’chifukwa chiyani anafunsa Eliya kuti: “Kodi mwabwera kudzandikumbutsa zimene ndinalakwitsa komanso kudzapha mwana wanga?” (1 Maf. 17:18; w14 2/15 15 ¶4-5) B
Chithunzi B
Zomwe Tikuphunzirapo
Yehova anaona mayi wamasiye ngakhale kuti ankakhala m’tauni imene anthu ankalambira Baala. Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani za Yehova komanso mmene tiyenera kuonera anthu am’gawo lathu? (Mac. 10:35)
Akhristu amene akukumana ndi mavuto azachuma, kodi angaphunzire chiyani pa chikhulupiriro komanso kulimba mtima kwa mayi wamasiye wa ku Zarefati? C
Chithunzi C
Kodi tingatsanzire kulimba mtima kwa mayi wamasiye wa ku Zarefati m’njira zinanso ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani mayi wamasiye wa ku Zarefati akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Mofanana ndi mayi wamasiye wa ku Zarefati, kodi tingasonyeze bwanji kuti timaona kuti ubwenzi wathu ndi Yehova ndi wofunika kuposa zinthu zakuthupi?
“Anthu Ovomerezeka ndi Mulungu Adzapeza Moyo Wosatha” (w11 2/15 13-17)
Onani umboni wakuti Yehova amachita chidwi ndi chilichonse chimene tachita chosonyeza chikhulupiriro, kaya chachikulu kapena chaching’ono.