29 ELIYA
“Mulungu Wanga Ndi Yehova”
BAIBULO silifotokoza mmene nkhani ya Eliya inayambira. Mbiri ya ufumu wa Isiraeli wa mafuko 10 inali yomvetsa chisoni chifukwa mafumu ake ankachita zinthu zoipa kwambiri. Ahabu anali mfumu ya nambala 7 pa mafumuwa ndipo Yehova ankamuona kuti anali woipa kwambiri kuposa mafumu ena onsewo. Ahabu anakwatira Yezebeli yemwe anali mwana wa mfumu. Ahabu ankalambira mafano ndipo mkazi wake ankalambira Baala zomwe zinkaphatikizapo kupereka nsembe ana. Choncho ankalimbikitsa mwamuna wake komanso Aisiraeli kuti azilambiranso Baala. Tsiku lina, Eliya anapita kwa Ahabu. Yehova anamutuma kuti akadzudzule mfumuyi komanso kuiuza za chiweruzo chake.
Kuti akafikitse uthengawu, ankafunika kuyenda ulendo wautali kuchoka ku Giliyadi kukafika ku Samariya. Sizinali zophweka chifukwa msewu wake unali wamiyala. Atafika ku Samariya, anapita kunyumba kwa Ahabu. Nyumbayi inkadziwikanso kuti “nyumba yaminyanga ya njovu,” mwina chifukwa cha mmene anaimangira. (1 Maf. 22:39) Yerekezerani kuti mukuona Eliya akulowa m’nyumba yomangidwa mogometsayi, atavala zovala zaubweya ndi lamba wachikopa akuima pamaso pa mfumu n’kumuuza kuti mulungu wawo Baala, ndi wopanda mphamvu. Mukuganiza kuti zinali bwanji ngati Yezebeli anali pompo n’kumva zimenezi? Kodi Ahabu ndi mfumukaziyi anamva bwanji? Zimene mneneri wolimba mtimayu ananena zinasonyeza kuti mulungu wawo yemwe ankamuona kuti angawagwetsere mvula, analibe mphamvu yochitira zimenezo. Ananena kuti Yehova agwetsa chilala m’dzikolo moti mvula siigwa kwa zaka zingapo kufikira pamene Eliyayo, yemwe anali mneneri wa Yehova, adzanene kuti mvula iyambiranso kugwa.
N’chiyani chinathandiza Eliya kulankhula molimba mtima? Tikhoza kupeza mbali ina ya yankho pa zomwe analankhula. Iye anayamba ndi kunena kuti: “Ndikulumbira m’dzina la Yehova Mulungu wamoyo, Mulungu wa Isiraeli amene ndimamʼtumikira.” Mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “amene ndimamʼtumikira” amatanthauza kuti “amene ndimakhala pamaso pake.” Eliya anaima pamaso pa mfumu yamphamvu. Koma mneneriyu ankadziwa mfundo yofunika yakuti amatumikira Yehova Mulungu choncho amaima pamaso pake. Mwina Ahabu ndi Yezebeli ankaoneka kuti ndi oopsa komanso amphamvu koma tikayerekezera ndi Yehova analibe mphamvu. Zimenezi ziyenera kuti zinathandiza Eliya kukhala wolimba mtima.
Eliya analimba mtima kukalankhula ndi mfumu komanso mfumukazi yoipa ndiponso Aisiraeli opanduka. Iye anadalira Yehova pamene ankachita mantha
Eliya anapitirizabe kusonyeza kulimba mtima pa utumiki umene Yehova anamupatsa. Iye anasonyeza zimenezi pamene anamvera Yehova n’kumakhala yekhayekha m’chigwa pa nthawi ya chilala ndi njala ndipo ankadalira madzi a mumtsinje komanso akhwangwala kuti azimubweretsera chakudya. Anasonyezanso kulimba mtima pamene Yehova anamutuma ku Sidoni komwe bambo ake a Yezebeli ankalamulira kuti akathandize mayi wina wamasiye yemwe anali ndi chikhulupiriro cholimba. Analimbanso mtima pamene anapita paphiri la Karimeli kukakumana ndi aneneri 450 a Baala. Iye anapereka umboni wakuti Yehova yekha ndi Mulungu woona. Dzina lakuti Eliya limatanthauza kuti “Mulungu Wanga Ndi Yehova” ndipo pa moyo wake wonse ankasonyeza kuti amadalira Yehova Mulungu wake.
Komabe, Eliya “anali munthu ngati ife tomwe.” (Yak. 5:17) Ankachita mantha ngati mmene aliyense amachitira. Pambuyo poti Yehova wachita zodabwitsa paphiri la Karimeli, Ahabu anakanitsitsa kusintha maganizo ake. Ndipo Yezebeli analumbira kuti apha Eliya moti mneneriyu anachita mantha. Iye anathawa poopa kuphedwa. Anali ndi nkhawa moti anauza Yehova kuti akufuna kufa. Ankadziona kuti ndi wosafunika ndipo ananena kuti sanali woposa makolo ake. Koma Yehova anamumvetsera moleza mtima. Patapita nthawi, kawiri konse Eliya anauza Mulungu kuti anali yekhayekha, ankachita mantha komanso ankaona kuti ntchito yake yapita pachabe. Yehova anatsimikizira mneneri wakeyu kuti sanali yekha komanso kuti anali wofunikabe. Yehova anamusankhiranso munthu woti azimuthandiza ndiponso kuti amuphunzitse ntchito pomukonzekeretsa kuti adzapitirize utumiki wake.
Pasanapite nthawi yaitali, Yehova anauza Eliya kuti apite kukafufuza Elisa. Onse awiri anapitiriza kutumikira Yehova ndi kupereka mauthenga pa nthawi yovuta kwambiri. Elisa anathandiza Eliya ndipo anaphunzira zambiri kwa iye. Mothandizidwa ndi Yehova, Eliya anakhalanso wolimba mtima ndipo anachita zimenezi kwa moyo wake wonse.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Eliya anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. N’chifukwa chiyani akhwangwala anali oyenerera kupereka chakudya kwa Eliya? (it “Khwangwala” ¶5-wcgr) A
Lior Kislev
Chithunzi A
2. Kodi Eliya anachita zodabwitsa ziti? (it “Eliya” Na. 1 ¶11-wcgr)
3. Paphiri la Karimeli, Eliya analamula anthu kuti athire madzi m’ngalande mpaka kudzadza. Pa nthawiyi kunali chilala, kodi madzi anawatenga kuti? (ba 17 ¶3) B
Todd Bolen/BiblePlaces.com
Chithunzi B: Chithunzi cha phiri la Karimeli ndi nyanja ya Mediterranean
4. Kodi chovala chauneneri cha Eliya chinkaimira chiyani, nanga n’chifukwa chiyani anachiponyera paphewa pa Elisa? (w14 2/1 12 ¶3)
Zomwe Tikuphunzirapo
Tikaganizira mmene Yehova anachitira zinthu ndi Eliya, kodi tingatani kuti abale ndi alongo athu azimasuka nafe akakumana ndi zokhumudwitsa? (1 Maf. 19:1-18) C
Chithunzi C
Eliya anaphunzitsa Elisa mofunitsitsa ntchito yomwe ankagwira. Kodi tingamutsanzire bwanji tikamaphunzitsa ena komanso kupatsa ena zochita?
Kodi tingatsanzire kulimba mtima kwa Eliya m’njira zinanso ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Eliya akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Onerani vidiyo yofotokoza mmene Yehova anathandizira Eliya kukwaniritsa utumiki wake.
Tengerani Chitsanzo cha Kuleza Mtima kwa Aneneri—Eliya: Gawo 1 (1:19)
Kodi achinyamata angaphunzire chiyani pa kulimba mtima komwe Eliya anasonyeza paphiri la Karimeli?
“Tetezani Kulambira Koona” (Nkhani zapawebusaiti “Zoti Muchite Pophunzira Baibulo”)