28 ASA
Anatumikira Yehova Ndi Mtima Wonse “kwa Moyo Wake Wonse”
MFUMU ASA inadabwa kwambiri ndi zimene inaona. Gulu la asilikali a Aitiyopiya linali m’dera la Ayuda pokonzekera kumenya nkhondo. Yehova anatumizapo anthu ake kunkhondo kambirimbiri koma palibe paliponse m’Baibulo pamene pamasonyeza kuti anakumanapo ndi gulu la asilikali lalikulu choncho. Asilikaliwo analipo 1 miliyoni koma Asa anali ndi asilikali pafupifupi 600, 000 okha. N’chiyani chinathandiza Asa kulimba mtima kukamenyana ndi gulu lalikulu chonchi?
Aka sikanali koyamba kuti Asa afunike kulimba mtima. Zaka 10 m’mbuyomo, atangoyamba kumene kulamulira ku Yuda, Asa ankachita zinthu mofanana ndi Mfumu Davide yemwe anali agogo a agogo ake. Mofanana ndi Davide, nayenso Asa ankafuna kusangalatsa Yehova Mulungu wake. Modzichepetsa, iye anamvera aneneri a Yehova, Odedi ndi mwana wake Azariya. Asa ali mwana analimba mtima kuchotsa zinthu zonse zoipa zimene anthu ankachita kungoyambira m’nthawi imene Mfumu Solomo inasiya kutumikira Yehova. Mwachitsanzo, anawononga mafano amene anthu ankalambira ndiponso anachotsa mahule aamuna apakachisi.
Asa anakonzanso zinthu zoipa zimene ngakhalenso anthu am’banja lake ankachita. Agogo ake aakazi a Maaka, anali ‘pa udindo wokhala mayi wa mfumu’ ku Yuda. Iwo anaimika fano lonyansa kwambiri lomwe n’kutheka kuti linkalimbikitsa anthu kugonana polambira. Asa ankaona kuti kukhala wokhulupirika kwa Yehova n’kofunika kwambiri kuposa kusangalatsa achibale ake. Choncho anachotsa agogo akewo pa udindo wawo n’kuwotchanso fanolo. Popeza Asa anasangalatsa Yehova, Yehovayo anadalitsa dzikolo ndipo linakhala pamtendere kwa zaka 10. Kodi Yehova anatani Asa ataukiridwa ndi gulu la asilikali a Aitiyopiya?
Mfumu Asa anakumana ndi gulu lalikulu la asilikali kuposa gulu lililonse lotchulidwa m’Baibulo
Asa atayang’ana m’chigwa cha Yuda anaona gulu la asilikali a Aitiyopiya, nthawi yomweyo anapemphera kwa Yehova. Taganizirani mmene asilikali ake anamvera pamene Asa anapemphera kuti: “Inu Yehova, zilibe kanthu kuti anthu amene mukufuna kuwathandizawo ndi ambiri kapena ndi opanda mphamvu. Tithandizeni Yehova Mulungu wathu chifukwa tikudalira inu, ndipo tabwera m’dzina lanu kudzamenyana ndi chigulu cha anthuchi. Inu Yehova ndinu Mulungu wathu. Musalole kuti munthu akuposeni mphamvu.” Yehova ayenera kuti anasangalala kwambiri ndi pemphero lokhudza mtima limeneli. Iye anaona kuti Asa ankachita zinthu ngati Yonatani, mwana wa Mfumu Sauli chifukwa onsewa ankaona kuti kwa Yehova, kuchuluka kwa asilikali n’kopanda kanthu. (1 Sam. 14:6) Aliyense amene ali kumbali ya Yehova, yemwe ndi wolamulira chilengedwe chonse, amapambana nthawi zonse ngakhale atakhala ochepa.
Asa anatsogolera asilikali ake kukamenya nkhondo. Ndiye kodi zinawayendera bwanji? Baibulo limati: “Yehova ndi gulu lake anawagonjetseratu.” Palibe msilikali aliyense amene anapulumuka.
Kenako Asa anapitiriza kulimbikitsa kulambira koyera. Ambiri mwa anthu a mu ufumu wa mafuko 10 wa Isiraeli omwe ankakhala kumpoto anasamukira kum’mwera kwa Yuda kuti azikalambira Yehova kukachisi wa ku Yerusalemu. Asa analumbiritsa Ayuda onse kuti adzakhale okhulupirika kwa Yehova.
Ngakhale zili choncho, nkhani ya Asa imafotokozanso zinthu zazikulu zimene analakwitsa. Pamene mfumu ya Isiraeli inaopseza kuti igonjetsa Yuda, Asa sanadalire Yehova kuti amuthandize. M’malomwake, anapereka ndalama kwa mfumu ya Siriya kuti iwathandize. Ndipo pamene Yehova anatumiza munthu wina wamasomphenya kapena kuti mneneri dzina lake Hanani kuti akamudzudzule, Asa anakwiya n’kulamula kuti aikidwe m’ndende. Atakalamba, Asa anadwala kwambiri ndipo m’malo mopempha thandizo kwa Yehova anafunafuna thandizo kwa ochiritsa. Zikuoneka kuti Asa sanapitirize kulimbitsa chikhulupiriro chomwe anali nacho poyamba.
Komabe, Yehova ndi Atate wachifundo. Ponena za zaka 41 zimene Asa analamulira, Baibulo limanena kuti: “Ngakhale zinali choncho, Asa anatumikira Yehova ndi mtima wonse kwa moyo wake wonse.” Nkhani ya Asa imatikumbutsa kuti Yehova amakonda anthu amene amamukonda. Imatikumbutsanso kuti sitiyenera kuiwala zimene Yehova watichitira. Ndipo chaka chilichonse tikamamutumikira n’kumaona zimene watichitira, chikhulupiriro chathu chidzalimba ndipo tidzapitiriza kukhala olimba mtima.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Asa anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Kodi “misanje” kapena kuti “mizati yopatulika” inali chiyani? Nanga ofukula zinthu zakale apeza umboni wotani wosonyeza kuti Aisiraeli ampatuko ankalambira mulungu yemwe mizatiyi inkaimira? (1 Maf. 15:12, 13; w08 6/1 9 ¶8–10 ¶4) A
Chithunzi A: Asa anachotsa agogo ake aakazi pa udindo ndipo anaphwanya mzati wopatulika
Chithunzi A: Asa anachotsa agogo ake aakazi pa udindo ndipo anaphwanya mzati wopatulika
2. Kodi zikuoneka kuti Hanani anali mwana wa ndani, nanga anatsanzira bwanji kulimba mtima kwa bambo ake? (it “Hanani” Na. 2-wcgr)
3. Ngakhale kuti Asa anachita zoipa zambiri, n’chiyani chikusonyeza kuti “anatumikira Yehova ndi mtima wonse”? (1 Maf. 15:14; w17.03 19 ¶5-6)
4. Kutentha mtembo sikunali kofala pakati pa Aisiraeli. Ndiye n’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti ‘pamaliro a Asa anawotchapo zinthu zambiri zonunkhira’? (2 Mbiri 16:14; w05 12/1 20 ¶5)
Zomwe Tikuphunzirapo
Zomwe mneneri Azariya analankhula zinalimbikitsa Asa kubwezeretsa kulambira koyera. Kodi mawu anu olimbikitsa angathandize bwanji anthu ena? B
Chithunzi B
Poyamba Asa anadalira Yehova pogonjetsa gulu lalikulu la asilikali koma pambuyo pake anadalira anthu kugonjetsa kagulu kochepa ka asilikali. Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani pa nkhani yodalira Yehova m’zochita zathu zonse? (Miy. 3:5, 6)
Kodi tingatsanzire bwanji kulimba mtima kwa Asa pa moyo wathu?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Asa akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Ngati mukukhala m’dziko lomwe mumalambira Yehova mwa ufulu, kodi mungatsanzire bwanji Asa pa mmene anagwiritsira ntchito nthawi yomwe anali pamtendere?
“Muzichita Zinthu Mwanzeru pa Nthawi Yomwe Zinthu Zikuyenda Bwino” (w20.09 14-19)
Onani mmene chitsanzo cha Asa chingatithandizire tikakumana ndi mayesero aakulu.
“Mudzapeza Mphoto Chifukwa cha Ntchito Yanu” (w12 8/15 8-10)