27 MEFIBOSETI
Sanakhumudwe Pamene Ankachitiridwa Zopanda Chilungamo
MEFIBOSETI anali mdzukulu wa Sauli, mfumu ya Isiraeli ndipo bambo ake anali Yonatani. Bambo akewa anali olimba mtima komanso okhulupirika kwa Yehova. Mnyamatayu ali ndi zaka 5 zinthu zinasintha kwambiri pa moyo wake. Agogo ake, a Sauli anavulala kwambiri pa nkhondo kenako anadzipha. Bambo ake, a Yonatani nawonso anaphedwa pa nkhondoyo. Mayi amene ankasamalira Mefiboseti atamva uthenga wochititsa manthawu, anamunyamula n’kuyamba kuthawa naye. Kenako mwanayo anagwa n’kuvulala kwambiri miyendo ndipo anakhala wolumala kwa moyo wake wonse.
Ngakhale kuti Mefiboseti ankakhala movutika kwambiri, iye sanakhumudwe nazo. Munthu wina wa ku Isiraeli dzina lake Makiri anamupezera malo okhala. Patapita nthawi, Mfumu Davide inakumbukira kuti inalonjeza mnzake wapamtima Yonatani kuti idzasamalira munthu aliyense wam’banja lake. (1 Sam. 20:14-17) Choncho Davide anaitanitsa Mefiboseti.
Mefiboseti anachita mantha chifukwa anali wam’banja la Mfumu Sauli yemwe anali woipa. Mwina ankaganiza kuti Mfumu Davide akufunanso kumupha. Komabe, iye anamvera n’kupita kwa mfumu. Davide analankhula naye mokoma mtima ndipo anamubwezera katundu yense wa agogo ake, a Sauli. Komanso anamuuza kuti ‘uzidya patebulo langa nthawi zonse.’ Mefiboseti anayamikira kwambiri ndipo ankadziona kuti sankayenera zinthu zimenezo moti anafunsa Davide chifukwa chake anamuchitira zimenezo. Iye ankadziona kuti ndi wosafunika kwenikweni moti anadziyerekezera ndi galu.
Mefiboseti ali mwana analumala, makolo ake anamwalira kenako anachitiridwa zinthu zopanda chilungamo
Patapita nthawi, zinthu sizinali bwino kwa Mefiboseti. Abisalomu anaukira bambo ake, Davide n’cholinga choti akhale mfumu ndipo anthu ambiri ankamuthandiza. Zimenezi zinapangitsa Davide kuti athawe ku Yerusalemu. Ziba yemwe anali wantchito wa Mefiboseti anasiya kumuthandiza chifukwa anapita kukathandiza Davide. Mefiboseti sanatsatire Davide koma anachita chinthu chomwe chinasonyeza kuti anali wokhulupirika kwa iye ndiponso kuti wakhudzidwa ndi zomwe zinachitikira Davideyo. Iye anasiya kumeta ndevu ngati mmene zimakhalira munthu akamalira maliro. Davide atagonjetsa Abisalomu anabwerera ku Yerusalemu. Komabe, Davide anakhumudwa ndi Mefiboseti. Chifukwa chiyani?
Pa nthawi imene Ziba anapita kukapatsa Davide chakudya, anamuuza bodza lokhudza Mefiboseti. Iye ananena kuti Mefiboseti anatsalira ku Yerusalemu poyembekezera kuti akhala mfumu. Tangoganizirani mmene Davide anamvera. Anali atachitidwa chipongwe osati ndi mwana wake yekha komanso Ahitofeli yemwe anali mnzake wokhulupirika komanso mlangizi wake. Mwina zimenezi zinachititsa kuti asavutike kukhulupirira kuti munthu winanso wamuchita chipongwe. Choncho analamula kuti cholowa chonse cha Mefiboseti chimene agogo ake, Mfumu Sauli anasiya chiperekedwe kwa Ziba.
Mefiboseti atamva bodza limene Ziba anauza Davide, anakonza zoti akakumane ndi Davideyo n’kumufotokozera zimene zinachitika. Davide anauza Mefiboseti kuti amuuze chifukwa chimene anatsalira ku Yerusalemu. Iye anafotokoza kuti sanapite nawo chifukwa chakuti ndi wolumala komanso kuti Ziba anamusiya osamutenga. Davide ayenera kuti anazindikira zoti Mefiboseti anasonyeza kuti anali ndi chisoni posiya ndevu zake zosameta. Zimenezi zinasonyeza kuti Mefiboseti sankafuna kuchitira chiwembu mfumu koma anali ndi nkhawa. Mulimonsemo, Davide anakhumudwa kwambiri ndipo sanafunenso kumva zambiri kuchokera kwa Mefiboseti. Kenako anaganiza zobweza malo ena kwa Mefiboseti. Iye ananena kuti Mefiboseti agawane malo a Sauli ndi Ziba.
Mefiboseti akanatha kukhumudwa poona kuti agawana malo ndi munthu amene anamunenera bodza kwa mfumu. Munthu akachitiridwa zopanda chilungamo, n’zosavuta kukwiya. (Deut. 19:18, 19) Pamafunika kulimba mtima kuti munthu aziganizira zokhazikitsa mtendere osati kumangodzimvera chisoni kapena kumangoganizira zoipa zimene ena amuchitira. Ndiye kodi Mefiboseti akanasankha kuchita chiyani?
Iye anayankha Davide modekha kuti: “Musiyeni [Ziba] atenge malo onsewo, kwa ine zili bwino chifukwa inu mbuyanga mfumu mwabwerera kunyumba yanu mwamtendere.” Chifukwa chakuti Mefiboseti anali wodzichepetsa ankaganizira kwambiri za mfumu yomwe inkaimira ulamuliro wa Yehova wachilungamo. Ngakhale kuti ena anamunenera mabodza komanso analanda katundu wake, iye anakhalabe wachimwemwe komanso anapitiriza kutumikira Mulungu mokhulupirika. Ngakhale kuti Mefiboseti sankamenya nawo nkhondo, iye anasonyeza kulimba mtima kuposa asilikali ambiri.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Mefiboseti anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Mefiboseti asanapite kwa Davide ankakhala “Mʼnyumba ya Makiri.” N’chiyani chikusonyezanso kuti Makiri anali wokhulupirika komanso wochereza? (2 Sam. 9:3, 4; it “Makiri” Na. 2-wcgr)
2. N’chifukwa chiyani Mefiboseti anadziyerekezera ndi “galu wakufa”? (2 Sam. 9:8; it “Galu” ¶5-wcgr) A
PhotoStock-Israel/Photodisc via Getty Images
Chithunzi A: Kale ku Isiraeli, agalu ankaonedwa ngati nyama zodetsedwa
3. Zomwe tikudziwa zokhudza Mefiboseti zikusonyeza bwanji kuti sakanalanda ufumu wa Davide? (w02 2/15 14 ¶11, mawu a m’munsi) B
Chithunzi B: N’kutheka kuti Yonatani anauza Mefiboseti za munthu yemwe Yehova anamusankha kudzakhala mfumu.
4. Kodi Yehova anadalitsa Mefiboseti m’njira ziti pambuyo pa zomwe zinamuchitikirazi? (it “Mefiboseti” Na. 2 ¶3-wcgr)
Zomwe Tikuphunzirapo
Anthu ambiri amavutika ndi nkhawa komanso mavuto ena omwe abale ndi alongo awo sangawamvetse bwinobwino. Kodi tikuphunzirapo mfundo ziti zolimbikitsa kuchokera kwa Mefiboseti?
Davide anapereka malo a Mefiboseti kwa munthu wina atangomva mbali imodzi ya nkhani. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira komanso kufufuza kaye nkhani yonse tisanasankhe zochita? C
Chithunzi C
Kodi tingatsanzire bwanji kulimba mtima kwa Mefiboseti pa moyo wathu?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Mefiboseti akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Onani mmene tingatsanzirire Mefiboseti tikaona kuti tachitiridwa zinthu zopanda chilungamo.
Kodi makolo angathandize bwanji mwana amene akudziona kuti sakondedwa ndi anthu ena?
“Kodi Umaona Kuti Ana Anzako Safuna Kucheza Nawe?” (w11 6/1 26-27)